‘Thokozani Mboni za Yehova Chifukwa cha Ufulu Wachipembedzo’
“MUSANATSEKE chitseko wa Mboni za Yehova akafika pakhomo panu, ganizani kaye za mazunzo ochititsa manyazi omwe akumana nawo posachedwapa, komanso zazikulu zomwe achita pa kukonzedwanso koyamba kwa malamulo okhudza ufulu wa anthu womwe tonsefe tikusangalala nawo.” Inatero nyuzipepala ya USA Today. Mboni za Yehova zinazunzidwa ku United States m’zaka zonse za m’ma 1940. Kukana kuchitira sawatcha mbendera, chinali chimodzi mwa zifukwa zake.—Eksodo 20:4, 5.
Milandu pafupifupi 30 yokhudza Mboni za Yehova inazengedwa m’bwalo lalikulu la U.S. Supreme Court pa zaka zisanu, kuchokera 1938 mpaka 1943. Nyuzipepalayo inati: “Kaŵirikaŵiri, Mboni zinali kudzutsa nkhani zomwe zinapangitsa kusintha malamulo koyamba (First Amendment) ndipo Woweruza Harlan Fiske Stone analemba kuti, ‘Mboni za Yehova ndizo zinathandiza pothetsa mavuto okhudza ufulu wa anthu.’”
Ndipo chakumapeto, nkhaniyo inati: “Zipembedzo zonse ziyenera kuthokoza Mboni za Yehova chifukwa cha kukula kwa ufulu [wachipembedzo].”
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Chithunzi cha Nyumba: Chochokera m’Khoti Lapamwamba ku United States, chojambulidwa ndi Josh Mathes; mmunsi kumanzere, oweruza: Chochokera m’Khoti Lapamwamba ku United States