Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w01 10/1 tsamba 32
  • Zomwe Tingaphunzire ku Mtengo wa Kanjedza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Tingaphunzire ku Mtengo wa Kanjedza
  • Nsanja ya Olonda—2001
Nsanja ya Olonda—2001
w01 10/1 tsamba 32

Zomwe Tingaphunzire ku Mtengo wa Kanjedza

INSAIKULOPEDIYA ina ya Baibulo imanena kuti kanjedza kapena kuti mgwalangwa “ndi mtengo wokongola mochititsa kaso.” M’nthaŵi za m’Baibulo ndiponso masiku ano, mitengo ya kanjedza imakongoletsa chigwa cha m’tsinje wa Nile ku Egypt ndiponso imapereka mthunzi wabwino m’malo a chinyontho a m’chipululu cha Negeb.

Mofanana ndi mitundu yake ina yambiri, mtengo wa kanjedza ndi wowongoka mochititsa chidwi. Mitengo ina imatalika mpaka mamita 30 ndipo imapitirizabe kubala zipatso kwa zaka 150. Inde, mtengo wa kanjedza ndi wokongola kwambiri ndiponso umabalanso zipatso modabwitsa. Chaka chilichonse mtengowu umatulutsa mikoko yambiri ya zipatso. Mkoko umodzi wokha umakhala ndi zipatso zopitirira 1,000. Ponena za zipatso za kanjedza, wolemba mabuku wina anati: “Anthu amene . . . anangodya zipatso zouma zokha za kanjedza za m’sitolo sangadziŵe mmene zaziŵisi zimakomera.”

Baibulo moyenerera limayerekezera anthu ena ndi mitengo ya kanjedza. Kuti munthu akhale wokongola kwa Mulungu monga mtengo wa kanjedza wobala zipatso, ayenera kukhala wowongoka mwamakhalidwe ndiponso ayenera kupitiriza kuchita ntchito zabwino. (Mateyu 7:17-20) Pachifukwa chimenechi, zithunzi za mitengo ya kanjedza zinali kukongoletsa m’kachisi wa Solomo ndiponso m’kachisi yemwe Ezekieli anaona m’masomphenya. (1 Mafumu 6:29, 32, 35; Ezekieli 40:14-16, 20, 22) Choncho, kuti kulambira kukhale kovomerezeka kwa Mulungu, wolambirayo ayenera kukhala ndi mikhalidwe yabwino monga ya mtengo wa kanjedza. Mawu a Mulungu amati: “Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa.”​—Salmo 92:12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena