Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w02 1/15 tsamba 32
  • Ntchito Zabwino Zimalemekeza Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ntchito Zabwino Zimalemekeza Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—2002
Nsanja ya Olonda—2002
w02 1/15 tsamba 32

Ntchito Zabwino Zimalemekeza Mulungu

AKRISTU oona amalemekeza Mulungu chifukwa cha khalidwe lawo labwino ndiponso ntchito zawo zopereka chitsanzo chabwino. (1 Petro 2:12) Zimenezi n’zimene zinachitika posachedwapa ku Italy.

Mu September 1997, chivomezi choopsa kwambiri chinawononga nyumba pafupifupi 90,000 m’madera osiyanasiyana a m’zigawo za Marche ndi Umbria. Magulu a Mboni za Yehova anathandiza mwamsanga okhulupirira anzawo ndiponso anthu ena. Anapereka makalavani, matenti ogonamo, zitofu, makina a mphamvu za magetsi, ndi katundu wina. Anthu anayamikira kwambiri zinthu zothandiza zimenezi.

Nyuzipepala ya Il Centro inalemba kuti: “Oyamba kufika ndi zinthu zothandizira anthu ovutika m’madera omwe anawonongedwa ndi chivomezicho anali a Mboni za Yehova a ku Roseto [m’chigawo cha Teramo] . . . Kuwonjezera pa kusonkhana nthaŵi zina kuti apemphere, anthu okhulupirika kwa Yehova amenewo anathandiza kwambiri anthu ovutikawo popanda kuganizira za chipembedzo chomwe ali.”

Woyang’anira tauni ya Nocera Umbra, yomwe inali imodzi mwa matauni omwe anawonongeka kwambiri ndi chivomezicho anathokoza Mboni mwa kulemba kuti: “Ndikukuthokozani ndi mtima wanga wonse chifukwa cha thandizo lanu lomwe munapereka kwa anthu a m’tauni ya Nocera. Ndikukhulupiriranso kuti anthu onse okhala m’tauni ino akuthokoza chimodzimodzi.” Ndiponso, Unduna wa za m’Dziko unapereka satifiketi yaulemu ndiponso mendulo ku Congregazione Cristiana dei Testimoni di Geova (Mpingo Wachikristu wa Mboni za Yehova) “kuchitira umboni ntchito yabwino ndiponso changu pothandizapo pa mavuto amwadzidzidzi m’zigawo za Umbria ndi Marche.”

Mu October 2000, madzi osefukira anawononga chigawo cha Piedmont kum’mwera kwa dziko la Italy. Kumenekonso, Mboni mwamsanga zinapita kukapereka thandizo. Anthu anayamikiranso kwambiri ntchito zabwino zimenezo. Chigawo cha Piedmont chinapereka mwala wachikumbutso wokongola kwambiri kwa Mboni za Yehova chifukwa cha “ntchito yotamandika yopanda malipiro yothandiza anthu a kumeneko omwe zinthu zawo zinawonongeka ndi madzi osefukirawo.”

Yesu Kristu analangiza ophunzira ake kuti: “Muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.” (Mateyu 5:16) Mboni za Yehova zikamachitira anthu omwe zimakhala nawo ‘ntchito zabwino’ zowathandiza mwauzimu ndiponso m’njira zina, zimalemekeza Mulungu ndi mtima wonse osati kudzifunira ulemu ayi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena