Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w02 6/15 tsamba 31
  • Nthaŵi Youlula Chinsinsi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nthaŵi Youlula Chinsinsi
  • Nsanja ya Olonda—2002
Nsanja ya Olonda—2002
w02 6/15 tsamba 31

Nthaŵi Youlula Chinsinsi

Kusunga chinsinsi pa nkhani zina kungathandize kuti pakhale mtendere ndipo ngati osatero pangakhale udani. Koma kodi pali nthaŵi youlula chinsinsi? Taonani zimene mneneri Amosi ananena za Mulungu wake. Anati: “Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.” (Amosi 3:7) Pamenepa tingaphunzirepo kanthu pa nkhani ya kusunga chinsinsi. Yehova angasunge chinsinsi pa nkhani zina kwa nthaŵi ina yake ndiyeno kenako angaulule kwa anthu ena. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pankhani imeneyi?

Nthaŵi zina, abusa oikidwa mumpingo wachikristu amaona kuti zimakhala bwino kusaulula nkhani zina zake. (Machitidwe 20:28) Mwachitsanzo, angasunge chinsinsi pa nkhani zokhudza makonzedwe ena kapena kusintha kwa maudindo mumpingo mpaka pa nthaŵi ina yake, poganizira mmene zimenezi zingathandizire mpingo.

Komabe ngati zitakhala choncho, anthu amene nkhaniyo ikuwakhudza n’kofunika kuwafotokozera bwinobwino ngati nkhaniyo adzaiulula, nthaŵi imene adzaiulule ndiponso mmene adzaiululire. Kudziŵa nthaŵi imene nkhaniyo adzaiulule kungawathandize kusungabe chinsinsi.​—Miyambo 25:9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena