“Anthu Aŵiri Anagogoda Pachitseko Chathu”
“PATHA zaka ziŵiri kuchokera pamene mwana wathu wamkazi anatisiya.” Inayamba choncho kalata imene inalembedwa mu nyuzipepala ya Le Progrès, ya ku Saint-Étienne ku France.
“Mélissa anali ndi miyezi itatu ndipo anadwala matenda oopsa otchedwa trisomy 18. Munthu sungaiŵale tsoka lopweteka kwambiri ngati limenelo. Ngakhale kuti tinaleredwa m’chipembedzo chachikatolika, tinali kuvutika ndi funso lakuti ‘Mulungu, ngati muliko, n’chifukwa chiyani mumalola zinthu ngati zimenezi kuchitika?’” Mwachionekere, mayi amene analemba kalata imeneyo anali wokhumudwa ndi wosowa pogwira. Kalatayo inapitiriza kuti:
“Zimenezi zitangochitika kumene, anthu aŵiri anagogoda pachitseko chathu. Nthaŵi yomweyo ndinazindikira kuti anali a Mboni za Yehova. Ndinatsala pang’ono kuwabweza mwaulemu, koma kenaka ndinaona bulosha limene amagaŵira anthu. Linali kufotokoza chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti anthu azivutika. Choncho ndinaganiza zowaloŵetsa m’nyumba n’cholinga chowathetsa makani. Ndinaganiza kuti pankhani ya kuvutika, banja langa ndiye linali litavutika kopitirira muyeso ndipo tinali titatopa kumva mawu osalimbikitsa amene anthu amakonda kunena oti ‘Mulungu anapatsa, ndipo Mulungu watenga.’ Amboniwo anakhala kwa nthaŵi yopitirira pang’ono ola limodzi. Anamvetsera mwachifundo, ndipo pamene amachoka, ndinamva bwino kwambiri moti ndinavomera kuti adzabwerenso. Zimenezi zinachitika zaka ziŵiri zapitazo. Pakadali pano sindinakhale wa Mboni za Yehova, koma ndinayamba kuphunzira nawo Baibulo, ndipo ndimapita ku misonkhano yawo monga momwe ndingathere.”