Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w04 9/1 tsamba 32
  • Zimene Mungachite Kuti Mulimbane ndi Kutaya Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mungachite Kuti Mulimbane ndi Kutaya Mtima
  • Nsanja ya Olonda—2004
Nsanja ya Olonda—2004
w04 9/1 tsamba 32

Zimene Mungachite Kuti Mulimbane ndi Kutaya Mtima

KODI mwataya mtima? Masiku ano pamene simungathe kudziŵa chimene chichitike m’tsogolo ndiponso zinthu n’zosokonekera kwambiri, anthu ambiri ataya mtima. Ena ataya mtima chifukwa sali pantchito. Enanso akulimbana ndi mavuto amene abwera chifukwa chakuti anachita ngozi. Ndipo ena akulimbana ndi mavuto a m’banja, matenda aakulu, kapena kusungulumwa.

Ngati mwataya mtima, kodi mungapeze kuti thandizo? Anthu ambiri padziko lonse lapansi alimbikitsidwa chifukwa choŵerenga Mawu a Mulungu, Baibulo. Amalimbikitsidwa ndi zimene ananena mtumwi Paulo, zoti: “Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Bwanji osaŵerenga mavesi ameneŵa ndi mavesi ena m’Baibulo lanu? Kuchita zimenezo ‘kudzalimbitsa mitima yanu ndi kukupatsani mphamvu.’​—2 Atesalonika 2:17, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono.

Kuyanjana ndi anthu amene amatumikira Yehova kungakuthandizeninso kulimbana ndi kutaya mtima. Lemba la Miyambo 12:25 limati: “Nkhaŵa iweramitsa mtima wa munthu; koma mawu abwino aukondweretsa.” Tikakhala pa misonkhano yachikristu, timamva “mawu abwino” amenewo, amene ali “otsekemera m’moyo ndi olamitsa mafupa.” (Miyambo 16:24) Bwanji osapita ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kukasonkhana nawo kuti mukadzionere nokha mmene msonkhano woterowo ungakulimbikitsireni?

Mungathandizidwenso ndi mphamvu ya pemphero. Ngati nkhaŵa za pamoyo zafika pothina, muuzeni “Wakumva pemphero” zonse zakukhosi kwanu. (Salmo 65:2) Mlengi wathu, Yehova Mulungu, amatimvetsa kuposa mmene timadzidziŵira eni akefe. Tingakhulupirire kuti adzatithandizadi. Mawu ake amatilonjeza kuti: “Um’senze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Indedi, “iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu.”​—Yesaya 40:31.

Yehova Mulungu watipatsa zida zamphamvu kwambiri zimene zingatithandize kulimbana ndi kutaya mtima. Kodi mukuzigwiritsa ntchito?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena