Munthu Wodzichepetsa wa ku Africa Kuno Amene Ankakonda Mawu a Mulungu
ALENDO obwera ku Africa kuno nthawi zambiri amadabwa kuona kuti sizivuta ngakhale pang’ono kuyambitsa nkhani ya m’Baibulo ndi anthu a kuno. M’posavuta kuti anthu achite chidwi ndi mafunso monga akuti, “Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?” kapena “Kodi pali njira iliyonse yothetseratu mavuto monga njala, matenda, nkhondo, ndiponso kuswa malamulo?” Anthu ambiri amalola kuti munthu wosam’dziwa awasonyeze mayankho a mafunsowa m’Baibulo. Kawirikawiri anthuwo amayamba kuphunzira Baibulo mokhazikika. Ndipo akamapita patsogolo m’zinthu zauzimu, amadzakhala Akristu obatizidwa.
Mmodzi wa anthu oyambirira a ku Africa kuno amene anachita zimenezi amatchulidwa m’Baibulo pa Machitidwe 8:26-40. Iyeyu anali wa ku Ethiopia ndipo anapita ku Yerusalemu kuti akalambire Mulungu woona, Yehova.
Monga mukuonera pachithunzipa, munthu wa ku Ethiopia ameneyu ankabwerera kwawo m’galeta lake, kwinaku atatsegula mpukutu n’kumawerenga. Ndiyeno munthu wina wosam’dziwa anam’peza n’kumufunsa kuti: “Kodi muzindikira chimene muwerenga?” Modzichepetsa, iye anavomereza kuti akufunika chithandizo ndipo anapempha munthu wosam’dziwa uja kuti akwere m’galetalo. Munthuyu dzina lake anali Filipo ndipo anali Mkristu wolengeza uthenga wabwino. Kenaka anamufunsa Filipoyo kuti alongosole tanthauzo la Malemba amene anali atangowerengawo. Filipo analongosola kuti malembawo anali ulosi wosonyeza imfa ya Mesiya, Yesu Kristu, yomwe inali itangochitika chaposachedwa. Filipo analongosolanso nkhani zina zokhudza “Uthenga Wabwino” wonena za Yesu, ndipo n’zosakayikitsa kuti zina mwa nkhanizi zinali zokhudza kuukitsidwa kwa Yesu.
Atamva nkhani zoona zochititsa chidwi zimenezi, munthu wa ku Ethiopia uja anafuna kukhala wophunzira wa Yesu ndipo anafunsa kuti: “Chindiletsa ine n’chiyani ndisabatizidwe?” Atabatizidwa, munthu wodzichepetsayu anapita kwawo ali wosangalala, ndipo Baibulo silinenaponso chilichonse za iye.
Masiku ano, Mboni za Yehova zikuthandiza anthu ambirimbiri padziko lonse kuphunzira za “Uthenga Wabwino” womwewu. Pakalipano, Mbonizi zikuchititsa maphunziro a Baibulo aulere a panyumba okwana pafupifupi sikisi miliyoni.