Mtengo Wokondwerera Chaka Chatsopano, Kodi Ndi Mwambo wa ku Russia Kapena Wachikristu?
“KUCHIYAMBI kwa zaka za m’ma 1830, anthu ankaonabe nkhani ya mtengo wosayoyola masamba monga ‘maganizo a ku Germany ongosangalatsa anthu.’ Pa mapeto a zaka khumi zimenezo, ‘unakhala mwambo’ m’nyumba za anthu olemera ku St. Petersburg. . . . Mu ma 1800, anali atsogoleri achipembedzo ndi anthu wamba okha amene sanatsatire mwambo woika mtengo wosayoyola masamba m’nyumba zawo. . . .
“Zaka za m’ma 1800 zisanafike, anthu sanakonde kwambiri . . . mtengowo. Malinga ndi mwambo wa ku Russia, amauona kukhala woimira imfa ndiponso ‘dziko la mizimu,’ mofanana ndi mwambo woika mtengowo padenga la nyumba zomwera mowa. Zimenezi sizinagwirizane ndi kusintha kwa maganizo a anthu kumene kunachitika pakati pa zaka za m’ma 1800. . . . N’zomveka kuti m’kupita kwa nthawi, mwambo wachilendowu unatanthauza zofanana ndi zimene mtengo wa pa Khirisimasi wa kumayiko a Kumadzulo umatanthauza, ndipo unagwirizana ndi nkhani ya Khirisimasi. . . .
“Kusintha mtengowu kukhala chizindikiro cha Chikristu ku Russia kunali ndi zopinga zake. A Tchalitchi cha Orthodox anatsutsa zimenezi. Atsogoleri achipembedzo anaona kuti mwambo watsopanowu unali wa ‘ziwanda,’ wachikunja, sunali wokhudzana ndi kubadwa kwa Mpulumutsi, ndiponso unali mwambo wochokera ku mayiko a Kumadzulo.”—Anatero Pulofesa Yelena V. Dushechkina, katswiri wa zachinenero pa yunivesite ya St. Petersburg State University.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Photograph: Nikolai Rakhmanov