Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w07 4/1 tsamba 32
  • Mungakhale Otetezeka M’dziko la Mavutoli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mungakhale Otetezeka M’dziko la Mavutoli
  • Nsanja ya Olonda—2007
Nsanja ya Olonda—2007
w07 4/1 tsamba 32

Mukuitanidwa ku Nkhani Yapadera Yakuti:

Mungakhale Otetezeka M’dziko la Mavutoli

Nkhani ya m’Baibulo imeneyi idzakambidwa padziko lonse m’mayiko opitirira 230. M’malo ambiri idzakambidwa Lamlungu, pa April 15, 2007. Kodi mudzaphunzirako zotani? Taganizirani mafunso ngati awa:

Kodi n’chiyani chikuchititsa anthu ambiri padziko lonse kuona kuti ndi opanda chitetezo?

Kodi ndi liti makamaka pamene anthu anayamba kuona kuti alibenso chitetezo?

Kodi n’kuti kumene anthu angapezeko chitetezo chenicheni ndipo angachipeze motani?

Dzapezeni mayankho a mafunso amenewa mwa kudzamvera nkhani yofunika kwambiri ya m’Baibulo imene idzakambidwe m’malo osiyanasiyana. M’malo ambiri nkhaniyi idzakambidwa pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. A Mboni a kwanuko adzakhala osangalala kukudziwitsani za nthawi ndi malo kumene nkhaniyi idzakambidwire. Tikukupemphani kuti mudzamvere nawo nkhani ya panthawi yake ndiponso yolimbikitsa imeneyi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena