Maphunziro Ofunika kwa Ana
GLADYS amagwira ntchito pasukulu ku Mendoza, m’dziko la Argentina. Tsiku lina akudutsa pa kalasi lina, anaona mphunzitsi akuwerengera ana ake a sitandade 4 Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo.a Gladys anauza mphunzitsiyo kuti iye ndi wa Mboni za Yehova ndipo anati angamuthandize mmene angagwiritsire ntchito bwino bukulo. Atamva zimene Gladys anafotokoza, mphunzitsiyo anasangalala ndipo anafuna kuti azigwiritsa ntchito bukulo kuphunzitsira ana a sukulu. Koma anafunikira kupempha kaye akuluakulu a sukulu. Anasangalala akuluakuluwo atalola.
Kenako, pa Tsiku Lolimbikitsa Kuwerenga Mabuku, mphunzitsiyo anakonza zoti ana ake awerenge mutu umodzi m’bukulo pamaso pa ana anzawo. Poona kuti mwambowu unali wothandiza kwambiri, mphunzitsiyo anapemphedwa kukalankhula pa TV. Pokambirana za khalidwe la ana a sukulu, wochititsa pulogalamuyo anafunsa mphunzitsiyo kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani ana m’kalasi lanu savuta?” Poyankha, mphunzitsiyo anafotokoza kuti amagwiritsa ntchito Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Ananena kuti ngakhale kuti saphunzitsa zachipembedzo m’kalasi lake, anali kugwiritsa ntchito bukulo kuphunzitsira ana makhalidwe monga ulemu, kulolerana, umodzi, kumvana, kumvera, ndi chikondi. Onse anavomereza kuti amenewa ndi maphunziro ofunika kwa ana.
Ngati mukufuna kuphunzitsa ana anu makhalidwe amenewa, pemphani Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kwa Mboni za Yehova.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.