Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w07 9/15 tsamba 32
  • ‘Kubala Zipatso Atakalamba’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Kubala Zipatso Atakalamba’
  • Nsanja ya Olonda—2007
Nsanja ya Olonda—2007
w07 9/15 tsamba 32

‘Kubala Zipatso Atakalamba’

ANTHU ambiri m’madera ozungulira nyanja ya Mediterranean amadzala migwalangwa pakhomo pawo. Mitengo imeneyi ndi yotchuka chifukwa cha kukongola kwake ndiponso zipatso zake zokoma. Komanso mitengoyi imabala zipatso kwa zaka zoposa 100.

Pofotokoza mwandakatulo maonekedwe a Msulami wokongola, Mfumu Solomo ya Isiraeli inati, Msulamiyo anali ngati mlaza, womwe ndi mtundu wina wa migwalangwa. (Nyimbo ya Solomo 7:7) Buku lina lofotokoza zomera zotchulidwa m’Baibulo lakuti Plants of the Bible limati: “Mawu a Chiheberi akuti mgwalangwa ndi ‘tàmâr.’ . . . Kwa Ayuda, mtengowu unali chizindikiro cha kukongola ndipo kawirikawiri dzina lake linkaperekedwa kwa akazi.” Mwachitsanzo, dzina la mchemwali wokongola kwambiri wa Solomo, yemwe anabadwa ku banja lina la bambo wake, linali Tamara. (2 Samueli 13:1) Mpaka pano, makolo ena amapatsabe ana awo aakazi dzina limeneli.

Si akazi okongola okha amene amayerekezedwa ndi migwalangwa. Wamasalmo anaimba kuti: “Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebano. Iwo ookedwa m’nyumba ya Yehova, adzaphuka m’mabwalo a Mulungu wathu. Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri.”​—Salmo 92:12-14.

Anthu amene amatumikira Mulungu mokhulupirika atakalamba, amafanana kwambiri ndi mtengo wokongola wa mgwalangwa. Baibulo limati: “Imvi ndiyo korona wa ulemu, idzapezedwa m’njira ya chilungamo.” (Miyambo 16:31) Ngakhale kuti mphamvu zawo zimachepa akamakula, okalamba angapitirizebe kukhala amphamvu mwauzimu mwa kuphunzira Baibulo lomwe ndi Mawu a Mulungu. (Salmo 1:1-3; Yeremiya 17:7, 8) Chifukwa cha mawu awo olimbikitsa komanso chitsanzo chabwino chimene Akhristu okalamba okhulupirika amapereka, ena amalimbikitsidwa ndiponso iwo amabalabe zipatso chaka ndi chaka. (Tito 2:2-5; Aheberi 13:15, 16) Mofanana ndi mgwalangwa iwo angapitirize kubala zipatso ngakhale kuti akalamba.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena