Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w07 10/1 tsamba 32
  • “Choonadi N’chiyani?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Choonadi N’chiyani?”
  • Nsanja ya Olonda—2007
Nsanja ya Olonda—2007
w07 10/1 tsamba 32

“Choonadi N’chiyani?”

KAZEMBE wachiroma Pontiyo Pilato ndiye anafunsa Yesu funsoli monyoza. Iye sankafuna yankho ndipo Yesu sanamuyankhe. Mwinamwake, Pilato ankaona kuti n’zosatheka kudziwa choonadi.​—Yohane 18:38.

Anthu ambiri masiku ano monga atsogoleri achipembedzo, aphunzitsi ndiponso andale ali ndi maganizo ngati a Pilato pankhani ya choonadi. Amakhulupirira kuti choonadi, makamaka pankhani ya makhalidwe ndi zinthu zauzimu, chimasinthasintha. Ngati zili choncho, ndiye kuti munthu aliyense angamasankhe yekha chabwino ndi choipa. (Yesaya 5:20, 21) Ndiponso, anthu angasiye kutsatira mfundo za makhalidwe abwino zimene makolo awo kale ankatsatira poganiza kuti tsabola wakale sawawa.

Tiyeni tione mawu amene anachititsa Pilato kufunsa funso limeneli. Yesu anali atanena kuti: “Chimene ndinabadwira, ndi chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi.” (Yohane 18:37) Yesu sankaona kuti n’zovuta kudziwa choonadi. Iye analonjeza ophunzira ake kuti: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”​—Yohane 8:32.

Kodi choonadi tingachipeze kuti? Panthawi ina, Yesu popemphera kwa Mulungu anati: “Mawu anu ndiwo choonadi” (Yohane 17:17) Baibulo ndi Mawu a Mulungu ndipo lili ndi choonadi chomwe chimapereka malangizo odalirika ndiponso chiyembekezo cha moyo wosatha.​—2 Timoteyo 3:15-17.

Pilato analibe chidwi chophunzira za choonadi. Nanga bwanji inuyo? Bwanji osafunsa Mboni za Yehova kuti mudziwe “choonadi” chimene Yesu ankaphunzitsa? Iwo angasangalale kukuuzani za choonadi chimenechi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena