Tsamba 32
◼ Tchulani zifukwa zinayi zotsimikizira kuti zimene Baibulo limalonjeza n’zoona. Onani tsamba 8.
◼ Kodi muyenera kulankhula motani ndi wachinyamata amene samayankha mafunso anu? Onani tsamba 12.
◼ Kodi makolo angatani kuti aphunzitse ana awo kukhala anthu oyamikira? Onani tsamba 13.
◼ Kodi Yesu ankatchula dzina la Mulungu polalikira Ayuda anzake? Onani tsamba 19.
◼ Kodi n’chiyani chinachititsa kuti munthu wina wa ku Mexico, amene anali m’gulu la zigawenga zotchedwa Ana a Satana, asinthe kwambiri pa moyo wake? Onani tsamba 28.