Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w09 11/15 tsamba 29
  • Kamtsikana Kowolowa Manja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kamtsikana Kowolowa Manja
  • Nsanja ya Olonda—2009
  • Nkhani Yofanana
  • “M’kamwa mwa Makanda”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • N’chifukwa Chiyani Anyamata Sandifunsira?
    Galamukani!—2010
  • N’chifukwa Chiyani Anyamata Samandifunsira?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Kodi Ndingachite Zotani Ngati Mtsikana Akundifuna?
    Galamukani!—2005
Nsanja ya Olonda—2009
w09 11/15 tsamba 29

Kamtsikana Kowolowa Manja

POSACHEDWAPA, kamtsikana kazaka 9 ku Brazil kanaganiza zogawa pawiri ndalama zimene kanasunga. Kanatenga madola 18 kukaponya m’bokosi la zopereka za mpingo ku Nyumba ya Ufumu. Ndipo kanatumiza madola 25 ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova, limodzi ndi kalata yachidule. M’kalatayo, kamtsikanaka kanalemba kuti: “Ndikupereka ndalama izi kuti zithandize pa ntchito yapadziko lonse. Ndikufuna kuthandiza abale ndi alongo ambiri padziko lonse lapansi kulalikira uthenga wabwino. Ndapereka ndalamazi ndi mtima wanga wonse ndiponso chifukwa chokonda kwambiri Yehova.”

Makolo a kamtsikanaka anakaphunzitsa kufunika kochita zonse zimene kangathe pa ntchito yolalikira Ufumu. Komanso anakathandiza kumvetsa kufunika ‘kolemekeza Yehova ndi chuma’ chimene kali nacho. (Miy. 3:9) Mofanana ndi kamtsikana kameneka, tiyeni tonse tikhale achangu popititsa patsogolo zinthu za Ufumu, m’dera lakwathu komanso padziko lonse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena