Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 10/1 tsamba 8-9
  • Kodi Ufumu wa Mulungu Udzakuchitirani Chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ufumu wa Mulungu Udzakuchitirani Chiyani?
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Ankaona Kuti Ufumu wa Mulungu Ndi Wofunika Kwambiri
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Ufumu wa Mulungu
    Galamukani!—2013
  • Sankhani Kukhala Kumbali ya Ufumu wa Mulungu Panopa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 10/1 tsamba 8-9
Banja likuphunzira zokhudza Ufumu wa Mulungu

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI UFUMU WA MULUNGU UDZAKUCHITIRANI CHIYANI?

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzakuchitirani Chiyani?

Monga taonera m’nkhani zapitazi, a Mboni za Yehova amaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri. N’kutheka kuti mwachita chidwi ndi zinthu zabwino zimene Ufumu wa Mulungu udzachite, zomwe zanenedwa m’nkhani zimenezi. Koma mwina mukukayikira ngati zimenezi zidzachitikedi.

Zimenezi n’zomveka, chifukwa si bwino kumangokhulupirira chilichonse. (Miyambo 14:15) Ndipotu Baibulo limanena za anthu ena a ku Bereyaa amene sankangokhulupirira chilichonse. Atauzidwa uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu, anthuwa sanafulumire kungokhulupirira zimene anamvazo. Iwo anafufuza kaye mosamala m’Malemba “kuti atsimikizire ngati zimene anamvazo zinalidi zoona.” (Machitidwe 17:11) Kunena kwina tingati, anthu a ku Bereya ankayerekeza zimene amva ndi zimene Malemba amanena. Ataona kuti zimene anamvazo n’zoona, anayamba kukhulupirira kuti uthenga wabwino unalidi wochokera m’Mawu a Mulungu.

Tikukulimbikitsani kuti nanunso muchite zofanana ndi zimenezi. A Mboni za Yehova amaphunzira ndi anthu Baibulo kwaulere ndipo zimenezi zimathandiza anthuwo kuti aone ngati zimene a Mboni amakhulupirira zokhudza Ufumu, zilidi zogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.

Kuwonjezera pa kudziwa zokhudza Ufumu wa Mulungu, kuphunzira Baibulo kungakuthandizeninso kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri awa:

  • Kodi anthufe tinachokera kuti?

  • N’chifukwa chiyani tili ndi moyo?

  • N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika?

  • Kodi dzikoli lidzawonongedwa?

  • Kodi n’chiyani chingathandize kuti banja likhale losangalala?

Komanso kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni ‘kuyandikira Mulungu’ kapena kuti kukhala naye pa ubwenzi. (Yakobo 4:8) Ubwenzi wanu ndi Yehova ukamalimba, mumayamba kudziwa kuti pali zambiri zimene Ufumu wa Mulungu ungakuchitireni panopa komanso m’tsogolo. Yesu anauza Atate wake m’pemphero kuti: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.

A Mboni za Yehova angaphunzire nanu Baibulo pogwiritsa ntchito buku ili.

Kuti mupeza munthu woti aziphunzira nanu Baibulo kwaulere, funsani a Mboni za Yehova kapena pitani pa webusaiti ya www.jw.org/ny. (Pitani pamene palembedwa kuti PEMPHANI MUNTHU WOTI AZIPHUNZIRA NANU, patsamba loyamba)

a Bereya unali mzinda wa ku Makedoniya wakale.

Folake Amakonda Kwambiri Ufumu wa Mulungu

Folake

Chaposachedwapa mtsikana wina wazaka 10, dzina lake Folake, anauzidwa ndi aphunzitsi ake kuti alembe nkhani ya mutu wakuti, “Chimene Ndimakonda Kwambiri Padzikoli.” Folake analemba kuti amakonda kwambiri kuuza anthu zokhudza Ufumu wa Mulungu ndipo anafotokoza chifukwa chake.

Iye ananena kuti: “Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni. Koma bomali ndi losaoneka choncho simungalione ngakhale mutavala magalasi.”

Folake analembanso zinthu zabwino zimene Ufumuwu udzachite, zomwe zimamusangalatsa kwambiri. Pofotokoza mavuto amene Ufumu wa Mulungu udzathetse, analemba kuti: “Zimandikhudza kwambiri ndikaona anthu osowa pokhala omwe amapezeka m’misewu” komanso “ana amene amafa ndi njala m’mayiko osiyanasiyana.” Folake anapitiriza kuti: “Koma ndimasangalala ndikawerenga lemba la Yesaya 65:21.” Ponena za anthu amene azidzalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu, lembali limati: “Adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.”

Folake ananenanso kuti amayembekezera nthawi imene Mulungu adzathetse matenda onse pogwiritsa ntchito Ufumu wake. M’nkhani yakeyi analembamo mawu a pa Chivumbulutso 21:4 omwe amati, Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” Pomaliza analemba kuti chinthu chimene amakonda kwambiri padzikoli, ndi kuuza anthu zokhudza Yehova ndi Ufumu wake. Apatu n’zoonekeratu kuti Folake amakonda kwambiri Ufumu wa Mulungu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena