Zamkatimu
January 2016
© 2016 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
3 Anadzipereka ndi Mtima Wonse—ku Oceania
MLUNGU WA FEBRUARY 29, 2016–MARCH 6, 2016
Kodi lemba la chaka cha 2016 ndi liti? Kodi tiyenera kuganizira chiyani tikamaona lembali m’Nyumba ya Ufumu? Nkhaniyi ikuyankha mafunso amenewa.
MLUNGU WA MARCH 7-13, 2016
12 Tiziyamikira ‘Mphatso Yaulere’ Imene Mulungu Anatipatsa
Mtumwi Paulo ananena kuti Yehova anatipatsa ‘mphatso yaulere, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.’ (2 Akor. 9:15) Kodi mphatsoyi ndi chiyani? Kodi imatithandiza bwanji kutsanzira Yesu Khristu, kukonda abale athu ndiponso kukhululukira ena ndi mtima wonse? Nkhaniyi ikuyankha mafunsowa komanso ikufotokoza zinthu zina zimene tingachite pa nthawi ya Chikumbutso.
MLUNGU WA MARCH 14-20, 2016
17 Mzimu Umachitira Umboni Limodzi ndi Mzimu Wathu
MLUNGU WA MARCH 21-27, 2016
Nkhani ziwirizi zikufotokoza mmene munthu amadziwira kuti wadzozedwa komanso zimene zimachitika akadzozedwa. Koma kodi odzozedwa ayenera kudziona bwanji? Nanga tiyenera kudandaula ngati chiwerengero cha anthu amene anadya zizindikiro pa Chikumbutso chakwera? Nkhanizi zikuyankhanso mafunso amenewa.
MLUNGU WA MARCH 28, 2016–APRIL 3, 2016
28 Timasangalala Kwambiri Kugwira Ntchito Limodzi ndi Mulungu
Kuyambira kale, Yehova wakhala akulola atumiki ake kuti azigwira naye ntchito pokwaniritsa cholinga chake. Iye akufuna kuti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse ndipo watipempha kuti tizigwira naye ntchitoyi. Nkhaniyi ikufotokoza madalitso amene timapeza chifukwa chogwira ntchito limodzi ndi Mulungu.
CHITHUNZI CHA PACHIKUTO:
MADAGASCAR
Mpainiya akulalikira munthu wina amene akuyendetsa ngolo mumsewu umene uli ndi mitengo ya malambe, mumzinda wa Morondava ku Madagascar
KULI OFALITSA
29,963
MAPHUNZIRO A BAIBULO
77,984
OPEZEKA PA CHIKUMBUTSO