Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA MAY 2-8, 2016
3 Achinyamata, Kodi Ndinu Okonzeka Kubatizidwa?
MLUNGU WA MAY 9-15, 2016
8 Achinyamata, Kodi Mungakonzekere Bwanji Kubatizidwa?
Timasangalala kwambiri kuona kuti chaka chilichonse anthu pafupifupi 250,000 amabatizidwa. Ambiri mwa anthuwa amakhala achinyamata ndipo ena amakhala asanakwanitse zaka 13. Kodi amadziwa bwanji kuti ndi okonzeka kudzipereka kwa Yehova? Nanga amakonzekera bwanji kuti ayenerere kubatizidwa? Nkhani ziwirizi zikuyankha mafunso amenewa.
MLUNGU WA MAY 16-22, 2016
13 Kodi Tingathandize Bwanji Kulimbitsa Mgwirizano Wathu?
Tikamayesetsa kuchita zinthu mogwirizana, Yehova amatidalitsa. Nkhaniyi ili ndi malangizo amene angatithandize kuti tizigwirizana mumpingo, m’banja komanso pogwira ntchito yolalikira.
MLUNGU WA MAY 23-29, 2016
18 Yehova Amatsogolera Anthu Ake Kuti Adzapeze Moyo
Yehova wakhala akutsogolera bwino anthu ake. Nkhaniyi ikufotokoza kuti iye amasintha malangizo amene amapereka kwa anthu ake kuti agwirizane ndi mmene zinthu zilili pa nthawiyo. Ikufotokozanso zimene tiyenera kuchita posonyeza kuti timafuna kuti Yehova azititsogolerera.