Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA JUNE 27, 2016–JULY 3, 2016
3 Kodi Mumathetsa Nkhani Mwachikondi Mukasemphana Maganizo?
Popeza tonsefe si ife angwiro, nthawi zina tingakhumudwitsane. Nkhaniyi ikufotokoza mmene mfundo za m’Baibulo zingatithandizire kuthetsa kusamvana.
MLUNGU WA JULY 4-10, 2016
8 “Pitani Mukaphunzitse Anthu a Mitundu Yonse”
Nkhaniyi ikusonyeza kuti a Mboni za Yehova okha ndi amene akukwaniritsa ulosi wa Yesu wa pa Mateyu 24:14. Ikufotokozanso zimene “asodzi a anthu” amachita.—Mat. 4:19.
MLUNGU WA JULY 11-17, 2016
13 Kodi Mumasankha Bwanji Zochita?
Kodi mumatani mukafuna kusankha zochita? Kodi mumangosankha zimene inuyo mukuona kuti n’zolondola? Kapena mumafunsa ena zimene iwowo akanachita? Nkhaniyi ikusonyeza kuti ndi bwino kusankha zochita mogwirizana ndi maganizo a Yehova.
MLUNGU WA JULY 18-24, 2016
18 Kodi Baibulo Likusinthabe Moyo Wanu?
Kodi mumaona kuti zikukuvutani kusintha zinthu zing’onozing’ono kusiyana ndi mmene munasinthira zinthu zikuluzikulu kuti muyenerere kubatizidwa? Nkhaniyi ikufotokoza chifukwa chake zimenezi zimachitika. Ikufotokozanso kuti Baibulo lingatithandize kuti tipitirizebe kukhala ndi makhalidwe osangalatsa Mulungu.
MLUNGU WA JULY 25-31, 2016
23 Kodi Zinthu Zonse Zimene Yehova Amatipatsa Zimakuthandizani?
Nkhaniyi itithandiza kudziwa kuti kupanda kusamala tingamanidwe zinthu zina zimene Yehova amatipatsa. Itithandizanso kudziwa zoyenera kuchita kuti zimenezi zisatichitikire.
28 Kale Lathu