Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w17 October tsamba 31
  • Anamusonyeza Kukoma Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anamusonyeza Kukoma Mtima
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Tingaphunzire Kwa “Wophunzira Amene Yesu Anali Kumukonda Kwambiri”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Kodi Yohane Analibe Chikhulupiriro?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Yohane Anasoŵa Chikhulupiliro?
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Yohane Yemwe Anali M’ndende Ankafuna Kumva Kuchokera kwa Yesu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
w17 October tsamba 31
John akulandira kabuku kofotokoza za uthenga wabwino wa Ufumu kuchokera kwa wa Mboni za Yehova

ANAMUSONYEZA Kukoma Mtima

BAMBO a mnyamata wina dzina lake John anabatizidwa chakumapeto kwa zaka za m’ma 1950 m’katauni kena ku Gujarat m’dziko la India. John, azichimwene ake, azichemwali ake komanso mayi ake anali akatolika olimbikira kwambiri ndipo ankadana ndi zimene abambo awo ankakhulupirira.

Tsiku lina, John anapemphedwa ndi bambo ake kuti akapereke kalata kwa mnzawo wina wa Mboni. Tsiku limenelo, John anadzicheka chala potsegula mgolo. Koma pofuna kumvera bambo akewo, anangomanga chalacho ndi kansalu kenakake n’kupita kukapereka kalatayo.

John atafika anapeza mkazi wa munthuyo yemwenso anali wa Mboni za Yehova. Polandira kalatayo, mkaziyo anaona kuti chala chake n’chovulala ndipo anamuuza kuti amuthandiza. Anatsuka balalo ndi mankhwala n’kulimanga bwinobwino ndi bandeji. Kenako anamupangira tiyi n’kumacheza naye nkhani zina zokhudza Baibulo.

Apa John anayamba kusintha maganizo ake odana ndi a Mboni. Iye anafunsa mkaziyo mafunso awiri okhudza nkhani zimene ankasiyana maganizo ndi bambo ake. Anamufunsa ngati Yesu si Mulungu komanso ngati Akhristu sayenera kupemphera kwa Mariya. Mlongoyo anagwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunsowo ndipo anakambirana naye m’chilankhulo chake chomwe ndi Chigujarati. Kenako anamupatsa kabuku kofotokoza za uthenga wabwino wa Ufumu.

Atawerenga kabukuko, John anazindikira kuti wapeza choonadi cha m’Baibulo. Iye anapita kwa wansembe n’kukamufunsanso mafunso awiri aja. Wansembeyo anapsa mtima kwambiri n’kumugenda ndi Baibulo uku akukalipa kuti: “Wasanduka Satana iwe eti? Tandiuze. Ndi pati m’Baibulo pamene amanena kuti Yesu si Mulungu? Nanga ndi pati pamene amati tisamalambire Mariya?” John anadabwa kwambiri ndi zimene wansembeyu anachita moti anamuuza kuti: “Sindidzapondanso mutchalitchi chachikatolika” ndipo anasiyiradi pomwepo kupita kutchalitchicho.

John anayamba kuphunzira ndi a Mboni ndipo anayamba kutumikira Yehova. Patapita nthawi, achibale ake ena anachitanso chimodzimodzi. Panopa John ali ndi chipsera pa chala chomwe anavulala zaka 60 zapitazo. Koma amakumbukira kuti kukoma mtima kumene anasonyezedwa pa nthawiyo kunamuthandiza kuti ayambe kulambira Yehova.​—2 Akor. 6:4, 6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena