Ntchito ya Kunyumba ndi Nyumba
Kodi tili ndi maziko a Malemba otani ochitira ntchito ya kunyumba ndi nyumba? Cholembedwa cha Uthenga Wabwino cha malangizo a Yesu kwa atumwi ake 12, ndipo pambuyo pake kwa alaliki 70, chimasonyeza bwino lomwe kuti anayenera kupita kunyumba ndi nyumba akumalalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. (Luka 10:1-7; Mat. 10:5-14) Ntchito yathu ya kunyumba ndi nyumba sili kokha yozikidwa pa Malemba komanso zipatso zake zimasonyeza kuti dalitso la Yehova lili pantchitoyo. Ndi chithandizo chachikulu koposa chotani nanga chomwe tili nacho cha bukulo Kukambitsirana za m’Malemba kaamba ka utumiki wakumunda! Ilo lili ndi mawu oyambitsira makambitsirano a Baibulo ndiponso chidziŵitso chothandiza pa Malemba ambiri kapena nkhani za chipembedzo. Chotero, musamangolinyamula komanso ligwiritsireni ntchito.