Zilengezo
◼ Chogaŵira cha June: Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. July: Mabrosha akuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? ndi Jehovah’s Witnesses in the Twentieth Century. Mipingo imene idakali ndi timabuku tamasamba 32 iyenera kugaŵira timeneti m’munda. August: Lililonse la mabrosha amasamba 32 otsatirawa lingagwiritsiridwe ntchito: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano,” Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, ndi Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? Kodi Mungachipeze Motani? September: Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. CHIDZIŴITSO: Mipingo imene idzafuna zinthu za mkupiti zotchulidwa pamwambazi iyenera kuzioda pa Literature Order Form (S-14) ya mwezi ndi mwezi yotsatira. Chonde musaode timabuku tamasamba 32, popeza kuti kulibeko ku Sosaite.
◼ October 29, 1994, lidzakhala Tsiku lapadera la Magazini. Chotero tikulimbikitsa mipingo yonse kutumiza maoda awo apadera a makope a October mwamsanga, kotero kuti adzatifike asanafike mapeto a July 1994.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina wake wosankhidwa ndi iye ayenera kuŵerengera maakaunti a mpingo pa June 1 kapena mwamsanga pambuyo pake monga momwe kungathekere. Perekani chilengezo ku mpingo pamene zimenezi zichitidwa.
◼ Zofalitsidwa Zomwe Zilipo:
Chicheŵa: Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Chingelezi: Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom; Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza; Kodi Mulungu Amatisamaliradi?; Jehovah’s Witnesses in the Twentieth Century; The Bible—Accurate History, Reliable Prophecy (kaseti ya vidiyo).