Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/94
  • Tsopano Ndiyo Nthaŵi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tsopano Ndiyo Nthaŵi
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndingakwanitse Bwanji Zolinga Zanga?
    Galamukani!—2010
  • Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndikwaniritse Zolinga Zanga?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Mmene Mungakwaniritsire Zolinga Zanu Zauzimu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
km 10/94

Tsopano Ndiyo Nthaŵi

1 Pamene mtumwi Paulo analemba kalata yake yachiŵiri kwa Akorinto, anawakumbutsa kuti iwo anali atatsimikiza mtima kuchita ntchito yabwino yopereka thandizo kwa okhulupirira anzawo ku Yerusalemu. Komabe, chaka chimodzi chinali chitapita, ndipo iwo anali asanatsirizebe ntchito imene inayambidwa. Chotero anawafulumiza kuti: “Pitirizani ndi kuimaliza: tsirizani ntchitoyo ndi kufunitsitsa komwe munali nako poilandira.”—2 Akor. 8:11, The New English Bible.

2 Panthaŵi ina yake, tonsefe tinadziikira zonulirapo. Tingakhale tinasankha kuwonjezera phande lathu mu utumiki wakumunda, kudziŵa abale athu bwino kwambiri, kuyenerera mwaŵi wa utumiki, kapena kugonjetsa chifooko china. Ngakhale kuti tinayamba ndi zolinga zabwino, mwina sitinayesetse kufikira chonulirapo chathu. Mosazindikira, milungu, miyezi, kapena ngakhale zaka zingakhale zitapita popanda ifeyo kupita patsogolo. Kodi kungakhale kwakuti tifunikira kugwiritsira ntchito uphungu wa ‘kupitiriza ndi kumaliza’ zimene tinayamba?

3 Kufikira Zonulirapo Zathu: Kupanga chosankha kuli kosavuta koma kukwaniritsa chosankhacho ndiko kovuta kwambiri. Kuzengereza kungalepheretse kupita patsogolo kulikonse. Tifunikira kusankha ndiyeno kutsimikiza mtima kuchita zimenezo mosazengereza. Kulinganiza kwa umwini kuli kofunika kwambiri. Nkofunika kupatula nthaŵi yofunikira kuchitira ntchitoyo ndi kutsimikizira kuti nthaŵiyo ikugwiritsiridwa ntchito pachifuno chimenecho. Nkwabwino kudziikira tsiku lomalizira ntchito ndiyeno kuchita modziletsa kutsimikizira kuti ntchitoyo ithe patsiku lomwelo.

4 Pamene kukhala kovuta kukwaniritsa zonulirapo zathu, nkosavuta kulingalira kuti: ‘Ndidzaziona nthaŵi ina.’ Koma sitidziŵa zimene zidzachitika mtsogolo. Miyambo 27:1 imati: “Usanyadire zamaŵa, popeza sudziŵa tsiku lina lidzabala chiyani.” Wophunzira Yakobo anachenjeza za kukhala ndi chidaliro chopambanitsa ponena za mtsogolo chifukwa “simudziŵa chimene chidzagwa maŵa. . . . Iye amene adziŵa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.”—Yak. 4:13-17.

5 Pokhala ndi zochenjeneketsa zambiri limodzinso ndi zimene ena amafuna kwa ife, zonulirapo zathu zingaiŵalidwe mosavuta. Pamafunikira kuyesayesa mwakhama kuti tizizikumbukira. Kutchula nkhaniyo m’mapemphero athu kuli kothandiza. Kupempha ena amene ali mabwenzi athu apamtima kutikumbutsa ndi kutilimbikitsa kungakhale kopindulitsa. Kuika zizindikiro pa kalenda yathu kudzatikumbutsa kupenda kupita kwathu patsogolo. Munthu ayenera kugamulapo ‘kuchita monga anatsimikiza mtima.’—2 Akor. 9:7.

6 Mwezi wa October ukupereka mpata wabwino wa kusumika maganizo pa zonulirapo zathu. Tidzakhala tikugaŵira masabusikripishoni a Galamukani! kapena Nsanja ya Olonda kapena a magazini onse aŵiri. Kodi tingaike zonulirapo zina zoyenera zimene tingazifikire? Bwanji ponena za kupeza sabusikripishoni imodzi yokha? Kugamulapo kuchita maulendo obwereza ambiri ndi kuyambitsa phunziro latsopano la Baibulo kungakhale zonulirapo zoyenera kwa ambiri.

7 Sikuli kwanzeru kukankhira kutsogolo chinthu chofunika, popeza kuti “dziko lapansi lipita.” (1 Yoh. 2:17) Mwaŵi wapadera ndi madalitso mu utumiki wa Yehova zilipo tsopano kaamba ka ife. Zili kwa ife kuzigwiritsira ntchito.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena