Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndi chisamaliro chotani chimene tiyenera kupereka pa ziŵiya zimene timagwiritsira ntchito mu ntchito ya umboni?
1 Ngakhale kuti wofalitsa mbiri yabwino angakhale ndi ulaliki wa m’Malemba woyenera m’maganizo, iye angakhale wosakonzekera ponena za ziŵiya zimene ayenera kugwiritsira ntchito. Pakhomo, iye angakhale alibe chogaŵira chatsopano. Magazini, mabrosha, ndi matrakiti amene ali m’chola chake cha mu umboni angakhale okwinyika kapena ong’ambika. Mwina sangakhoze kupeza pensulo kapena cholembapo cha kunyumba ndi nyumba chifukwa chakuti za m’chola chake sizili m’dongosolo labwino. Nkofunika kusamalira kwambiri ziŵiya zanu musanapite mu utumiki wakumunda.
2 Kodi ndi zinthu ziti zimene chola cha mu umboni chokonzedwa bwino chiyenera kukhala nazo? Baibulo nlofunika kwambiri. Phatikizanimo zolembapo za kunyumba ndi nyumba. Tsimikizirani kuti mwanyamula chofalitsa chimene chikugwiritsiridwa ntchito mweziwo. Makope atsopano a magazini, limodzi ndi matrakiti ndi mabrosha, ngofunikanso. Nyamulani buku la Kukambitsirana. Kukhala ndi Utumiki Wathu Waufumu watsopano kudzakulolani kupenda maulaliki osonyezedwa musanapite pakhomo. Pamene mukugwira ntchito m’ndime imene mungapezemo anthu achinenero chakunja, kungakhale bwino kukhala ndi kabuku ka Good News for All Nations. Kukhala ndi kope la china cha zofalitsa zathu chonena za achichepere kudzakuthandizani kukhala wokonzekera kulankhula ndi achinyamata.
3 Chilichonse chogwiritsiridwa ntchito chiyenera kuikidwa mwadongosolo m’chola chanu. Chola sichitofunikira kukhala chatsopano, koma chiyenera kukhala chaudongo ndi chooneka bwino. Chola chanu cha mu umboni chili mbali ya ziŵiya zanu zogwiritsira ntchito polengeza mbiri yabwino. Chisungeni mwaudongo.