Zilengezo
◼ Mabuku ogwiritsira ntchito mu April ndi May: Sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda. June: Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? kapena buku lina lililonse la masamba 192. July ndi August: Lililonse la mabrosha otsatirawa a masamba 32 angagwiritsiridwe ntchito: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndi “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” CHIDZIŴITSO: Mipingo imene sinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambapa iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Request (S-AB-14) yotsatira ya mwezi ndi mwezi.
◼ Monga momwe kunalengezedwera papitapo, Uthenga wa Ufumu wapadera udzatulutsidwa pa Sande, April 23, pamisonkhano ya mpingo, limodzinso ndi pamisonkhano yadera ndi masiku a msonkhano wa padera, imene idzachitika patsikulo. Kugaŵira Uthenga wa Ufumu kuyenera kuyamba utatulutsidwa. Zimenezi zikukhudza mipingo YONSE, kuphatikizapo ija imene ingafunikire kusintha misonkhano yawo chifukwa cha misonkhano yaikulu, kucheza kwa woyang’anira dera, kapena zochita zina. Mipingo imene idzakhala ndi nkhani yapadera pambuyo pa April 23 ingatulutse ndi kuyamba kugaŵira Uthenga wa Ufumu pa April 24.
◼ Kwa oyang’anira otsogoza: Tikupemphani kutumiza ku Sosaite zokumana nazo zilizonse zapadera zimene mpingo wanu wakhala nazo m’chaka chino, kuphatikizapo zokumana nazo za utumiki wa upainiya wothandiza ndi tsiku la magazini lapadera, April 1, 1995. Tikufuna kudzasankha chokumana nacho chabwino koposa cha m’munda wathu choika m’lipoti la chaka. Chonde zitumizeni mosapyola pa July 1, 1995.
◼ Chonde kumbukirani nthaŵi zonse kulemba dzina la mpingo ndi nambala yake pa S-AB-14 ndi kusayina fomuyo patsamba lomaliza. Tikulandira mafomu ambiri opanda dzina ndi nambala choncho sitingadziŵe eni ake kusiyapo kungowawononga kuno zimene zili zachisoni popeza mpingo sudzalandira mabuku omwe unaoda.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Chicheŵa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso; Mboni za Yehova—Zikuchita Chifuniro cha Mulungu Mogwirizana pa Dziko Lonse Lapansi. Chingelezi: Imbirani Yehova Zitamando (Laling’ono); 1995—Yearbook of Jehovah’s Witnesses. Tumbuka: Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!