Konzekerani Chikumbutso
Kodi aliyense, kuphatikizapo mlankhuli, wadziŵitsidwa za nthaŵi yeniyeni ndi malo a chochitikacho? Kodi mlankhuli akudziŵa kuti programuyo siyenera kuposa mphindi 45?
Kodi pali amene wasankhidwa kupeza zizindikiro zake? (Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1990, masamba 16-18.) Kodi makonzedwe a kulinganiza thebulo loyalidwapo nsalu yaudongo ndi matambula ndi mbale zake zokwanira apangidwa?
Kodi makonzedwe a kuyeretsa Nyumba Yaufumu pasadakhale ndi pambuyo pake apangidwa? Kodi akalinde ndi oyendetsa zizindikiro asankhidwa? Kodi msonkhano wa kuonana nawo kuti afotokozeredwe ntchito zawo wachitidwa? Kodi ndi njira zotani zimene zidzatsatiridwa kuti mutsimikizire kuti zizindikirozo zafika kwa onse mokwanira?
Kodi makonzedwe a kuthandiza abale ndi alongo okalamba ndi odwala kufikapo apangidwa? Ngati pali aliyense wa odzozedwa amene angakhale wobindikiritsidwa ndi wosakhoza kupezekapo, kodi makonzedwe a kumperekera zizindikiro apangidwa?