Nthaŵi Zonse Pali Zochita Zochuluka
1 Anthu a Yehova ali anthu otanganitsidwa. Nthaŵi zonse pali “zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye.” (1 Akor. 15:58, NW) Pali misonkhano yampingo ya mlungu ndi mlungu imene tiyenera kukonzekera ndi kufikapo. Tikulimbikitsidwa kusalola mlungu uliwonse kutha popanda kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda. Nthaŵi yokwanira iyenera kupatulidwa kaamba ka phunziro laumwini ndi phunziro labanja. Akulu ndi atumiki otumikira ali ndi ntchito zambiri zampingo. Nthaŵi zina timapemphedwa kuthandiza osoŵa oyenerera thandizo. Kuwonjezera pa zonse zimenezi, tili ndi mathayo ambiri mogwirizana ndi banja lathu, kuntchito, ndi kusukulu.
2 Panthaŵi zina, ena a ife tingathedwe mphamvu ndi zonse zimene tiyenera kuchita. Komabe, anthu otanganitsidwa kwambiri angakhale pakati pa anthu achimwemwe kwambiri ngati mkhalidwe wachikatikati ndi kaonedwe ka zinthu koyenera zisungidwa.—Mlal.3:12, 13.
3 Mtumwi Paulo anali mmodzi wa awo amene anali ndi zochita zochuluka. Anagwira ntchito zolimba kuposa atumwi ena. Anagwira ntchito mosatopa monga mlaliki, akumalalikira poyera ndi kunyumba ndi nyumba, pamenenso sananyalanyaze mathayo ake monga mbusa wa gulu la nkhosa. Kuwonjezera pa mathayo onsewo anasamalira zosoŵa zake mwa kugwira ntchito yakuthupi monga wosoka mahema. (Mac. 20:20, 21, 31, 34, 35.) Mosasamala kanthu za kutanganitsidwa kwake, Paulo anali wofunitsitsa nthaŵi zonse kuchita zowonjezereka mu utumiki wa Yehova.—Yerekezerani ndi Aroma 1:13-15.
4 Paulo anasunga uchikatikati wake ndi mtima wachimwemwe mwa kudalira Yehova kaamba ka nyonga. Anaona utumiki wake kukhala wofupa ndi wokhutiritsa. (Afil. 4:13) Anadziŵa kuti Mulungu sadzaiŵala ntchito yake. (Aheb. 6:10) Chisangalalo cha kuthandiza ena kudziŵa Yehova chinampatsa mphamvu. (1 Ates. 2:19, 20) Chitsimikiziro cha kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chake chozikidwa m’Baibulo chinamsonkhezera kukhalabe wakhama.—Aheb. 6:11.
5 Tiyenera kulingaliranso za zotulukapo zabwino za ntchito yathu. Kukhalapo kwathu ndi kukhala ndi phande m’misonkhano kumamangirira ndi kulimbikitsa ena. (Aheb. 10:24, 25) Zoyesayesa zathu zakhama kufikira anthu onse ndi uthenga wabwino zimachirikiza kupita patsogolo kwa mpingo pamene chikondwerero chikula ndipo atsopano asonkhana nafe. (Yoh. 15:8) Kuthandiza ena osoŵa kumachirikiza mzimu wogwirizana kwambiri mumpingo wonga wa m’banja. (Yak. 1:27) Ndiponso, monga Paulo, sitiyenera konse kuiŵala kuti kukhala otanganitsidwa m’ntchito zopindulitsa kumakondweretsa Yehova Mulungu. Timaona kumtumikira kukhala mwaŵi waukulu. Kwa ife kulibe njira ina yabwino kwambiri kuposa imeneyi!
6 Kukhala ndi zochita zochuluka kulinso ndi phindu lina. Pamene tili otanganitsidwa ndi kutsata njira yabwino yauzimu yochitira zinthu, nthaŵi imaonekera kukhala ikupita mofulumira. Pozindikira kuti tsiku lililonse limene likupita limatidzetsa pafupi ndi dziko latsopano, timalandira mokondwa moyo wotanganitsidwa, popeza kuti tilibenso nthaŵi ya kulondola zinthu za dziko zopanda pake.—Aef. 5:15, 16.
7 Ndithudi, pali zochita zochuluka mu ntchito ya Ambuye. Koma tingakhalebe achimwemwe ngati tipitiriza kudalira pa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu, amene amapangitsa utumiki wathu kukhala wotsitsimula ndi wofupa.—Mat. 11:28-30; 1 Yoh. 5:3.