Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu May: Mkupiti wa sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda. June: Knowledge That Leads to Everlasting Life. July ndi August: Lililonse la mabrosha otsatirawa amasamba 32: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndi “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”. Pamene kuli koyenera, mabrosha monga Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Our Problems—Who Will Help Us Solve Them?, ndi Will There Ever Be a World Without War? angagaŵiridwe.
◼ Nyumba za Ufumu: Mipingo imene ikufuna kupeza malo, kulemba mapulani, kupeza ndalama, kapena kuchita chilichonse kuti amange Nyumba ya Ufumu, ikupemphedwa kuti iyambe yalembera Sosaite pa Box 30749, Lilongwe 3, popeza Sosaite ingakhale ndi uphungu wothandiza umene ingapereke. Mipingo ija imene yamanga nyumba zokumaniramo kuyambira pamene chiletso cha Mboni za Yehova chinachotsedwa ikupemphedwa kulembera ku Sosaite ndi kufotokoza zimene akwanitsa kumanga.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Mabaundi Voliyumu a Watchtower a 1953–1955—Chingelezi