Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu June: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. July ndi August: Lililonse la mabrosha otsatirawa amasamba 32: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndi “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”. Pamene kuli koyenera, mabrosha monga Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Our Problems—Who Will Help Us Solve Them?, ndi Will There Ever Be a World Without War? angagaŵiridwe. September: Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Ngati palibe gaŵirani, Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? kapena Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina wosankhidwa ndi iye ayenera kuŵerengera maakaunti a mpingo pa June 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Perekani chilengezo kumpingo zimenezi zitachitidwa.
◼ Pakali kusoŵa kwa otembenuza Chicheŵa ndi Chitumbuka. Ngati mukufuna kufunsira ndipo muli ndi zaka zakubadwa pakati pa 19 ndi 35, mbeta ndi wobatizidwa mosachepera pa chaka chimodzi ndipo muli wofunitsitsa kugwira ntchito kwachikhalire pa Beteli, chonde lemberani ku Translation Department, Watch Tower Society, Box 33459, Lusaka, 10101, Zambia.
◼ Kuyambira m’June, mabaji a msonkhano wachigawo wa 1996 adzaphatikizidwa pa mabuku otumizidwa. Sikudzakhala kofunikira kuti muwaode. Malinga ndi ukulu wa mpingo uliwonse, mabajiwo adzatumizidwa m’maunyinji a 25. Nkofunika kuoda mapulasitiki a mabaji kaamba ka aliyense wofuna mumpingo.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha—Chicheŵa
Mabaundi Voliyumu a Watchtower ndi Awake! a 1995—Chingelezi
New World Translation of the Holy Scriptures (Deluxe lamthumba; DLbi25), lakuda kapena lofiira—Chingelezi
Watch Tower Publications Index 1986-1990—Chingelezi