Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu July ndi August: Lililonse la mabrosha otsatirawa amasamba 32: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndi “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”. Pamene kuli koyenera, mabrosha monga Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Our Problems—Who Will Help Us Solve Them?, ndi Will There Ever Be a World Without War? angagaŵiridwe. September: Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Mipingo imene ili ndi Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi kapena Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe m’stoko ingagaŵire mabuku ameneŵa. October: Sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda kapena ya Galamukani! kapena ya magazini onsewo.
◼ Misonkhano Yachigawo: Onse amene akulinganiza kukaloŵa Msonkhano Wachigawo wa 1996 ku Thete, akulangizidwa za malo amsonkhano atsopano osinthidwa kukhala ku Linthipe I. Madeti ake sanasinthe.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha—Chicheŵa
New World Translation of the Holy Scriptures (Deluxe laukulu wapakati; DLbi12), lofiira—Chingelezi
Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki—Chingelezi