Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndi misonkhano iti ya mpingo imene iyenera kuchitidwa mkati mwa mlungu wa msonkhano wadera?
Msonkhano wokha umene mipingo iyenera kuuchita m’mlungu wa msonkhano wadera ndiwo Phunziro la Buku la Mpingo. Misonkhano ina inayi imaloŵedwa m’malo m’njira ina ndi programu ya msonkhano wadera. Makonzedwe ameneŵa adzathandiza aliyense wa ife kukonzekerera ndi kulinganiza zinthu pasadakhale kaamba ka programu ya kudyetsedwa imene yakonzedwa kaamba ka ife ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.—Mat. 24:45-47; Sal. 122:1; 93:5.