Bokosi la Mafunso
◼ Kodi muyenera kuchitanji pamene wokamba nkhani yapoyera sanafike panthaŵi yake pamisonkhano?
Nthaŵi zina, mikhalidwe yosapeŵeka ingalepheretse mbale kufika panthaŵi yake kudzapereka nkhani yake. Ngati mukudziŵa kuti adzafika posapita nthaŵi, akulu angasankhe kuyamba ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda; Msonkhano Wapoyera ungatsatire pambuyo pake. Bwanji ngati kwaonekeratu kuti wokamba nkhani sadzabwera? Mwinamwake mmodzi wa okamba nkhani apamalopo angapereke nkhani iliyonse imene anakonzekera.
Kukonzekera mosamala pasadakhale kaŵirikaŵiri kumapeŵetsa vutoli. Mgwirizanitsi wa nkhani zapoyera ayenera kulankhula ndi wokamba nkhani aliyense mlungu umodzi pasadakhale kuti amkumbutse za gawo lake. Chikumbutsocho chiyenera kuphatikizapo nthaŵi ya misonkhano, keyala ndi nambala ya foni ya Nyumba ya Ufumu, ndi malangizo osavuta a mmene angapezere holoyo. Wokamba nkhani ayenera kulemba mosamalitsa zinthu zofunika zimenezi. Ayenera kuona gawo lake mwamphamvu, akumasintha zochita zake zaumwini mofunikira kotero kuti akwaniritse thayo limeneli. Ngati chinachake chosapeŵeka chimene chidzamlepheretsa kuchita motero chachitika, ayenera kulankhula ndi mgwirizanitsi wa nkhani zapoyera nthaŵi yomweyo kotero kuti aikepo wina. Muyenera kuyesayesa mwamphamvu kuti mupeŵe kusintha zinthu nthaŵi itatha kale. Ngati wokamba nkhani wagwidwa ndi zina zake ndipo adzachedwa kwa mphindi zingapo, ayenera kuimba foni ku Nyumba ya Ufumu kotero kuti abale adziŵe chochita.
Kuyamikira magawo a nkhani zapoyera, kukonzekera bwino kwa pasadakhale ndi zikumbutso, ndi kuyang’anira mosamalitsa zingachititse mpingo kumakhala ndi nkhani yapoyera yopindulitsadi mlungu uliwonse.