Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/96 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 10/96 tsamba 7

Zilengezo

◼ Zogaŵira za mu October: Sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda kapena ya Galamukani! kapena ya magazini onse aŵiri. November: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Kuyesayesa kwapadera kudzachitidwa kubwerera kulikonse kumene tinagaŵira zofalitsa, ndi cholinga cha kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. December: New World Translation ndi buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? January: Buku lililonse la masamba 192 lofalitsidwa 1984 isanafike limene mpingo ungakhale nalo m’stoko monga Happiness—How to Find It, “Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo, Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano, ndi “Let Your Kingdom Come.” Ameneŵa angagaŵiridwe pa chopereka cha nthaŵi zonse cha K12.00. Mipingo imene idakali ndi Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe kapena Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona ingagaŵire ameneŵa pa mtengo wobwezedwa wa K6.00. Ngati mipingo ilibe ameneŵa m’stoko angaodedwe ku Sosaite pa Literature Request Form (S-AB-14) yanthaŵi zonse.

◼ Mphatika m’kope lino la Utumiki Wathu Waufumu ndi “Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1997” ndipo iyenera kusungidwa kaamba ka kuonamo mu 1997 yense.

◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—1997 pa oda yawo ya mabuku ya October. Timabukuto tidzakhalako m’Chicheŵa, ndi m’Chingelezi. Mpaka pamene timabukuti tidzakhalapo ndi kutumizidwa, tidzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mpambo wolongedzera katundu wa mipingo. Timabuku ta Kusanthula Malemba ndi zinthu za oda yapadera.

◼ Mipingo ina yatumiza makalata kapena malipoti ku Sosaite popanda kuikapo masitampa pa maenvulopu. Choncho potenga makalata otero ku ofesi ya positi, Sosaite imalipiritsidwa. Tikudziŵitsa mipingo kuti ngati kalata ilibe masitampa ndipo Sosaite ilipira, ndalamayo idzaikidwa ku akaunti ya mabuku ya mpingo. Chotero, chonde tsimikizirani kuti sitampa yaikidwa pa kalata musanaitumize, kapena siyani kalata yanu pa malo a Sosaite osiyira katundu kuti idzatengedwe.

◼ Zofalitsa Zatsopano Zomwe Zilipo:

Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha—Chifrenchi

Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu—Chingelezi

Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja—Chicheŵa, Chifrenchi

Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?—Chicheŵa, Chifrenchi

Mabaundi Voliyumu a Watchtower a 1958-59—Chingelezi

◼ Makaseti Omvetsera Omwe Alipo:

Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?—Chingelezi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena