Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu November: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Kuyesayesa kwapadera kudzachitidwa kubwerera kulikonse kumene tidzagaŵira zofalitsa, ndi cholinga cha kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. December: New World Translation ndi buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? January: Buku lililonse la masamba 192 lofalitsidwa 1984 isanafike limene mpingo ungakhale nalo m’stoko. Mipingo imene ilibe mabuku ameneŵa ingagaŵire Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano. February: Gaŵirani buku lililonse lakale la masamba 192 limene muli nalo m’stoko.
◼ Mipingo imene ikali ndi Uthenga wa Ufumu Na. 34 ingalimbikitse ofalitsa kuugaŵira monga momwe amachitira ndi matrakiti ena, kaya kukhomo ndi khomo kapena kumalo ena. Ngati zili zololeka, ofalitsa angasiye umodzi panyumba iliyonse yopanda anthu, akumatsimikizira kuti auika posaonekera kwa odutsa. Tiyenera kuyesayesa kugaŵira makope otsala a uthenga umenewu wofunika.
◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda 1997 Yearbook of Jehovah’s Witnesses pa oda yawo ya mabuku ya November. (Onani Mpambo wa Zofalitsa za Watch Tower, ndime 8.) Yearbook idzakhalako m’Chingelezi. Mpaka pamene Yearbook idzakhalapo ndi kutumizidwa, idzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mpambo wolongedzera katundu wa mipingo. Ma Yearbook ndi zinthu za oda yapadera.
◼ Tikufuna kukumbutsa mipingo kuti pamene mafomu autumiki atumizidwa ku mipingo ayenera kulipiriridwa ndi thumba la mpingo. Ndiponso muyenera kukumbukira kuti pamene titumiza mtokoma wa makhadi a medical directive, wofalitsa aliyense amene wapatsidwa khadi ayenera kuchita chopereka kotero kuti mpingo ulipirire ndalama zolembedwa pa invoisi. Kulephera kutumiza ndalama za mafomu a utumiki ndi makhadi a medical directive, kwaipitsa maakaunti a Mabuku a mipingo ina.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Mboni za Yehova m’Mozambique—Mbiri ya Kusunga Umphumphu (Brosha lolongosola zochita za Mboni za Yehova m’Mozambique mofanana ndi Yearbook yachingelezi ya 1996)—m’Chicheŵa mokha
Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!—Chicheŵa