Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu May: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? June: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Sumikani maganizo pa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. July ndi August: Lililonse la mabrosha a masamba 32 otsatirawa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira ndi Sangalalani ndi Moyo Padziko Lapansi Kosatha!
◼ Kuyambira May, mabaji achingelezi a msonkhano wachigawo wa 1997 azatsagana ndi mitokoma ya mabuku. Simutofunikira kuwaodetsa. Malinga ndi ukulu wa mpingo uliwonse, tidzatumiza mabajiwo m’maunyinji a 25. Ngati mipingo ikufuna mabaji ena, ingaodetse pa Literature Request Form (S-14). Muyenera kuodetsa mapulasitiki a mabaji ngati ena mumpingomo akuwafuna.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Yearbook of Jehovah’s Witnesses ya 1997 (Mtengo wapadera wa K3.60 kwa ofalitsa ndi K2.40 kwa apainiya)—Chingelezi
Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?—Chingelezi