Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu December: New World Translation ndi buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? January: Buku lililonse la masamba 192 lofalitsidwa 1985 isanafike lomwe mpingo uli nalo m’sitoko. Mipingo yomwe ilibe mabuku amenewo ingagaŵire brosha lakuti “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” February: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha kapena buku lililonse la masamba 192 limene mpingo ungakhale nalo m’sitoko. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wasatha. Khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.
◼ Mipingo ingayambe kuoda mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! m’Chingelezi limodzi ndi oda yawo ya mabuku ya December. (Onani Mpambo wa Zofalitsa za Watchtower, ndime 6-8, 10.) Mabaundi voliyumu adzapezeka m’Chingelezi. Pampambo wolongedzera mabuku a mpingo tidzalembapo kuti, “Zoyembekezeredwa,” kenako mabaundi voliyumuwo akadzakonzedwa tidzakutumizirani. Mabaundi voliyumu ngofuna oda yapadera.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina amene iye wamsankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa December 1 kapena padeti lina koma lapafupi. Mutatha zimenezo lengezani ku mpingo.
◼ Chikumbutso cha mu 1999 chidzakhalako Lachinayi, pa April 1, dzuŵa litaloŵa. Takudziŵitsani zimenezi pasadakhale kuchitira kuti abale athe kupezeratu nyumba zimene angafune, ngati kuli koti pali mipingo ingapo yomwe imagwiritsira ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi ndiponso kuti mwina mungafune kupezeratu malo ena. Akulu ayenera kudzavomerezana ndi eni malowo kuti atsimikizire kuti sipadzakhala zochitika zina zododometsa pamalopo, kuti programu ya Chikumbutsoyo idzachitike mwa mtendere ndi mwa dongosolo. Popeza kuti chochitikacho nchapadera, posankha wokamba nkhani ya Chikumbutso, bungwe la akulu liyenera kusankha mkulu wina yemwe alidi wokhoza bwino kwenikweni, osati kumangosinthana kapena osati chaka chilichonse azingokamba munthu mmodzimodziyo.
◼ Mabaibulo achicheŵa tsopano ali pamtengo wa K50.00.
◼ Chonde dziŵani kuti manambala atsopano a telefoni ku ofesi ya Sosaite ku Lilongwe, ndi 782392; Fax ndi 731285.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
◼ Ma 1997 Yearbook of Jehovah’s Witnesses (Pamtengo wa K3.60. Chonde dziŵani kuti ma 1998 Yearbook adzakhala pamtengo wanthaŵi zonse wa K18.00—Chingelezi
Mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda a 1951-1996—Chingelezi
Mabaundi voliyumu a Galamukani! a 1984, 1991-96 (Mabaundi voliyumu onse a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ali pamtengo wa K72.00 imodzi.)—Chingelezi