Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu February: “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano” March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wasatha. Khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April: ndi May: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki apende ntchito ya apainiya onse okhazikika. Ngati pali wina yemwe zikumvuta kukwanitsa maola ofunikawo, akulu amthandize. Onaninso malingaliro ena m’makalata a Sosaite (S-201) ya October 1, 1993, ndi ya November 1, 1992. Ndiponso onani ndime 12-20 m’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wachingelezi wa October 1986.
◼ Ngati papereŵera ndalama zina pa akaunti yamagazini ya mpingo wanu, potumiza masabusikripishoni ku Sosaite, chonde tumizaninso fomu ya M-203, masilipi a sabusikripishoni, S-20 ndi ndalama. Sonyezani pa S-20 kuti ndalama za masabusikripishoni. Mukapanda kutumiza ndalama pomwe mpingo wanu wapereŵeza ndalama, masabusikripishoniwo sakonzedwa.
◼ Ngati pali chizindikiro cha kuchotsa (-) pa sitetementi yanu yamwezi ndi mwezi yochokera ku Sosaite, zimenezo sizikutanthauza kuti muli ndi ndalama za Sosaite, koma kuti Sosaite ili ndi ndalama zanu. Ena amafunsira kuti pangongole yawo patsala ndalama zingati chifukwa chosadziŵa zimenezi.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
“All Scripture Is Inspired of God and Beneficial”—Chingelezi
Mboni za Yehova m’Zaka za Zana la Makumi Aŵiri—Chicheŵa, Chingelezi
Mboni za Yehova ndi Maphunziro—Chicheŵa, Chingelezi
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako—Chicheŵa, Chingelezi
Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira—Chicheŵa
“Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”—Chicheŵa, Chingelezi
Uthenga wa Ufumu Na. 35—Chicheŵa, Chingelezi, Chitumbuka