Kodi Misonkhano Yathu Yachikristu Mumaiona Bwanji?
1 Kodi misonkhano yachikristu njofunika motani kwa inu? Kodi nkofunika motani kwa Yehova kuti anthu ake azisonkhana pamaso pake nthaŵi zonse? Kodi mumaona misonkhano monga mmene iye amaionera? Amatiuza mmene amaonera mbali imeneyi ya kulambira kwathu pa Deuteronomo 4:10. (Ŵerengani.) Misonkhano yachikristu ili mbali yofunika yakulambira kwathu Yehova.
2 Yehova ankatsogolera misonkhano imeneyo kupyolera mwa angelo ake oyera. Koma lero akuchita nafe kudzera mwa mngelo wake wamkulu wamphamvu wokhala pampando wachifumu kudzanja lake lamanja. Nchifukwa chake “tiyenera kusamaladi zimene tidazimvazi. . . . Pakuti ngati mawu adalankhulidwa ndi angelo adakhala okhazikika, . . . tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero, [popeza kuti chinayamba kulankhulidwa kupyolera mwa Ambuye?, NW]. (Ahebri 2:1-4) Tikaona malangizo athu ochokera kumwamba monga mmene Mulungu amafunira kuti tiwaone, nzosadabwitsa kuti mtumwi Paulo akutilangiza moyenerera kuti tisamaleke kusonkhana kwathu pamodzi, “monga amachita ena.”—Aheb. 10:25.
3 Kodi inunso mumamva choncho ponena za kusonkhana ndi abale anu pamisonkhano yachikristu? Kodi inu mumachita bwanji pankhani imeneyi? Kodi mumapezeka pamisonkhano yonse, kuphatikizapo Phunziro la Buku la Mpingo? Kapena mumaona kuti mumazoloŵera kuphonya misonkhano? Kodi misonkhano ili ndi malo otani m’moyo wanu? Kodi mumalimbikitsa ena kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse?
4 Mosasamala kanthu zoti zochita zathu za tsiku ndi tsiku nzotani, uphungu wa Paulo sunganyalanyazidwe. Ngakhale kuti mpomveka kuti Mkristu nthaŵi zina angaphonye msonkhano chifukwa cha matenda kapena mikhalidwe ina imene sangathe kuisintha, chimenecho sichiyenera kungokhala chizoloŵezi chake. (Aroma 2:21) Poti tili ndi ntchito zambiri zofuna kuchita, kuphatikizapo zingapo zateokrase, Mkristu afunikira kudziŵa kuti zofunika kwambiri nziti. (Afil. 1:10) Misonkhano imaphatikizidwa pa zinthu zofunika kwambiri kwa Mkristu ndipo njofunika kuti tizikula mwauzimu. Kusamvera lamulo lakuti tizipezeka pamisonkhano yachikristu nkoopsa ndipo zotsatirapo zake zingakhale zangozi kwa mtumiki wa Yehova.
5 Muzilimbikitsana wina ndi mnzake kupezeka pa phunziro la buku la mpingo: Pa Maphunziro a Buku a Mpingo ena pamapezeka anthu oŵerengeka ndithu. Kodi mumakhalapo nthaŵi zonse pamsonkhano umenewu? Ngati mukuti iyayi, mwakhala mukuphonya kanthu kena kofunika. Phunziro la buku ndiyo imodzi mwa njira zimene Yehova amatisamalira. (1 Pet. 5:7) Amafuna kuti tipite patsogolo m’chidziŵitso ndi panzeru kuti tilimbe mwauzimu. Koma kwinaku, Satana angakonde kutichedwetsa kuti tisakule msanga mwauzimu ndi kutifooketsa kuti tisakhale ofunika kwenikweni kwa Yehova ndi gulu Lake. Musalole zimenezo kuchitika! Lekani mzimu wachifundo ndi wachikondi wopezeka pakagulu ka anthu kameneka ukusonkhezereni kutamandabe Yehova.—Yerekezerani ndi Salmo 111:1.
6 Pamene Paulo analembera Aroma, anati ankalakalaka kuwaona. Chifukwa? Kuti awagaŵire mtulo wina wauzimu kuti ‘akhazikike,’ [“alimbikitsike,” NW]. (Aroma 1:11) Anaona kuti kusonkhana nkofunika, indedi, kofunikira, pakuti anapitiriza kuti: ‘Kuti tilimbikitsane.’ Kapena malinga ndi mawu amtsinde a Reference Bible: “Kuti tonse tilimbikitsidwe.” (Aroma 1:12) Nayenso Paulo, wokhala mtumwi, anazindikira kuti anafunikira chilimbikitso kudzera m’misonkhano yachikristu.
7 Aliyense mumpingo angapindule kwambiri ndi Phunziro la Buku la Mpingo. Nthaŵi zina, limapereka mapindu omwe sangabwere mwachindunji kudzera m’makonzedwe ena a mpingo. Nchifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa chakuti aliyense wopezekapo amasamalidwa payekhapayekha ndipo pali mipata yambiri yoti munthu ayankhepo kuposa mmene zimakhalira pamisonkhano yaikulu. Nthaŵi zambiri, limaphunzitsa munthu kulengeza poyera chikhulupiriro chake pamisonkhano ina ngakhalenso mu utumiki wakumunda, popeza kuti pa Phunziro la Buku la Mpingo ndiwonso malo okumanira popita ku utumiki wakumunda.
8 Kusamvera lamulo lakuti tizipezeka pamisonkhano yachikristu nkoopsa ndipo zotsatirapo zake zingakhale zangozi kwa mtumiki wa Yehova. Tsopano kuposa ndi kale lonse, tiyenera kugwiritsitsa chikhulupiriro chathu ndi kufulumiza ena ku chikondano ndi ntchito zabwino. Sitikufuna kuzoloŵera kuleka kusonkhana kwathu pamodzi. Tiyenera kulimbikira kulimbikitsa ena ndi kuwathandiza, kuphatikizapo achatsopano, kuti azipezeka pamisonkhano nthaŵi zonse. Tikamatero, tidzasonyeza kuti timakonda ena ndi kutinso timayamikira misonkhano yathu yachikristu.