Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/98 tsamba 1
  • Tonsefe Timafunikira Kuthandizana Kuti Ntchito Igwirike

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tonsefe Timafunikira Kuthandizana Kuti Ntchito Igwirike
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukukwaniritsa Mbali Zonse za Utumiki Wanu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • “Pitani Mukaphunzitse Anthu a Mitundu Yonse”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • “Mubale Chipatso Chambiri”
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kudzipereka Ife Eni Mwaufulu Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 6/98 tsamba 1

Tonsefe Timafunikira Kuthandizana Kuti Ntchito Igwirike

1 Wophunzira aliyense wa Yesu Kristu ayenera kudziŵa kuti kuyesayesa kwake kuchirikiza ntchito yolalikira Ufumu ndi kutengamo mbali nkofunika kwambiri. Yesu anazindikira kuti ophunzira ake azidzabala zipatso za Ufumu mosiyanasiyana. (Mat. 13:23) Ngakhale kuti ntchito yaikulu yolalikira ikuchitidwa ndi apainiya olimbikira, onse amene akupitirizabe mofunitsitsa kulemekeza Mulungu mwa kubala zipatso zambiri mmene angathere, ayenera kuyamikiridwa.—Yoh. 15:8.

2 Kugwirira Ntchito Pamodzi Kumakwaniritsa Zambiri: Yesu ananeneratu kuti ophunzira ake pomadzagwirira ntchito pamodzi, ntchito zawo zidzaposa zake. (Yoh. 14:12) Kaya mikhalidwe yathu imatilepheretsa kuchita zambiri kapena imatilola kuwonongera nthaŵi yambiri pa kulalikira Ufumu, tonsefe ndife ofunika kuti ntchitoyo igwirike. Zangokhala mongadi mmene Paulo ananenera, kuti: “Thupi lonse, lokowanidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiŵalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi.”—Aef. 4:16.

3 Ena angaganize kuti sakuchita zambiri. Komabe, m’maso mwa Yehova chinthu chofunika nchakuti utumiki wathu ukhale wa mtima wonse. Chilichonse chimene timamchitira nchamtengo wapatali ndipotu amachiyamikira.—Yerekezerani ndi Luka 21:1-4.

4 Chirikizanibe Ntchitoyo: Tonsefe tili ndi mwayi wochirikiza mwakuthupi ntchito ya padziko lonse imeneyi. Ena angathandizenso mwa kugwira ntchito ndi manja pochirikiza ntchito ya Ufumu imeneyi. Aliyense angayesetse kukonzekera bwino kukayankha pamisonkhano ndi kukakhala ndi mbali mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Tikamagwiritsira ntchito mipata yolimbikitsa ena, tingathandize mpingo kukulitsa mkhalidwe wauzimu, ndipo zimenezo zimauthandiza kuti ukhoze kugwira ntchito imene unapatsidwa.

5 Inde, tonsefe timafunikira kuthandizana kuti ntchito igwirike. Wina asamaganize kuti ngwosafunikira. Zimene timachitira pamodzi potumikira Yehova, kaya nzambiri kapena zochepa, zimatisiyanitsa ndi ena onse monga alambiri oona a Mulungu. (Mal. 3:18) Aliyense wa ife angachite mbali yofunika pakulemekeza Yehova ndi kuthandiza ena kumdziŵa ndi kumtumikira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena