Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/98 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 8/98 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu August: Mungagwiritsire ntchito lililonse la mabrosha otsatirawa a masamba 32: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Mabrosha akuti Buku la Anthu Onse, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Our Problems—Who Will Help Us Solve Them?, ndi Will There Ever Be a World Without War? mungawagaŵire pamene kuli koyenera. September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. October: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kumene tapeza anthu ochita chidwi, tingagaŵire masabusikripishoni paulendo wobwereza. November: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.

◼ Mtokoma wokwanira wa mafomu oti agwiritsiridwe ntchito m’chaka chautumiki cha 1999 ukutumizidwa kumpingo uliwonse. Gwiritsirani ntchito mafomuwa mwanzeru. Ayenera kugwiritsiridwa ntchito kokha pachifuno chake.

◼ Mpingo uliwonse udzalandira mafomu atatu a Kuŵerengera Mabuku (S-AB-18). Mlembi wampingo ayenera kukumana ndi mtumiki wamabuku kuchiyambiyambi kwa August ndi kusankha tsiku loti adzaŵerengere mabuku amene mpingo uli nawo pamapeto pa mweziwo. Mabuku onse amene ali m’sitoko ayeneradi kuŵerengedwa, ndipo ziwonkhetso zake zilembedwe pafomu ya Kuŵerengera Mabuku. Tengani chiŵerengero cha magazini amene alipo kwa mtumiki wamagazini. Tumizani kope loyamba ku Sosaite pasanafike pa September 6. Sungani kope lakaboni m’fayelo yanu. Kope lachitatulo mungaligwiritse ntchito ngati poyambira kuŵerengako. Kuŵerengeraku kuyenera kuyang’aniridwa ndi mlembi, ndipo fomu yodzazidwayo ipendedwe ndi woyang’anira wotsogoza. Mlembi ndi woyang’anira wotsogoza asaine fomuyo.

◼ Mipingo ingayambe kuoda ma Kalenda a Mboni za Yehova a 1999 pa fomu yawo yoodera mabuku ya September. Makalenda adzakhalako mu Chicheŵa ndi Chingelezi.

◼ Komiti Yautumiki ya Mpingo iyenera kusamalira mwamsanga mafomu onse ofunsira utumiki waupainiya wokhazikika. Komiti yautumiki siyenera kusunga fomuyo pofuna kuona ngati wofunsirayo angakwanitse chiŵerengero cha maola ofunikawo. Tsiku loikidwa lingasinthidwe ngati mafomu alandiridwa tsiku lopemphedwalo litadutsa. Sizitheka kuika munthu paupainiya kuyambira ndi tsiku la m’mbuyo kokha ngati pali zifukwa zomveka bwino. Ngati zifukwa zoterozo zilipo, tumizani fomuyo pamodzi ndi kalata.—Onani mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa October 1986, ndime 24-6.

◼ Tidzaphunzira mabrosha angapo pa Phunziro la Buku la Mpingo. Mu Utumiki Wathu Waufumu wa June 1998 kunalengezedwa kuti kuyambira mlungu wa September 21, 1998, tidzakhala tikuphunzira brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Pambuyo pa kuphunzira limeneli, tidzaphunzira lakuti Tawonani! Ndikupanga zinthu zonse Zatsopano kenako lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Ochititsa maphunziro a buku ayenera kukonza mafunso pankhani zimene zilibe mafunso. Panthaŵiyi, tidzalekeza kaye kuphunzira buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona.

◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:

Mabaundi voliyumu a Galamukani! a 1984, 1991-1997—Chingelezi

Mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda a 1951-1985, 1989, 1991, 1993, 1995, ndi 1997—Chingelezi

◼ Makompakiti Disiki Atsopano Omwe Alipo:

Kingdom Melodies No. 8

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena