Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/98 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 11/98 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu November: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. December: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. January: Lililonse la mabuku a masamba 192 limene mpingo ungakhale nalo lofalitsidwa isanafike 1985. Mipingo imene ilibe mabuku ameneŵa ingagaŵire buku lakuti Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani? kapena Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. February: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.

◼ Mipingo ingayambe kuoda ma Yearbook of Jehovah’s Witnesses a 1999 pa oda yawo ya mabuku ya November. Ma Yearbook adzakhalako m’Chingelezi mokha. Mpaka pamene ma Yearbook adzakhalapo ndi kutumizidwa, adzaonekera ngati “Zoyembekezeredwa” pa ndandanda yolongedzera mabuku ya mipingo. Ma Yearbook ndi zinthu za oda yapadera.

◼ M’zaka zaposachedwapa, pakhala mipata yabwino yopita kukayenda m’maiko akunja. Pachifukwachi, abale athu ambiri akonza zokacheza kumaiko ena. Kaŵirikaŵiri, amapempha chidziŵitso ku maofesi a nthambi za Sosaite. Maofesi a nthambi amakhala osangalala kupereka maadiresi a Nyumba za Ufumu ndi nthaŵi za misonkhano kuti zithandize pofufuza mipingo ya kumaloko. Ndiponso, angapereke malangizo a mmene angakachezere ku ofesi ya nthambiyo. Komabe, malipoti akusonyeza kuti pamakhalanso kufunsa zambiri monga ngati za kayendedwe, malo ogona, malo ochititsa chidwi ndi nkhani zina zofanana ndi zimenezi. Maofesi a nthambi sakhala ndi chidziŵitso choterechi, ndiponso alibe nthaŵi yopereka chidziŵitsocho. Alendo akulimbikitsidwa kufufuza zimenezi kwina monga ngati ku mabungwe a zamaulendo, kapena mabungwe okopa alendo amene mwachizoloŵezi amapatsa alendo chidziŵitsochi.

◼ Nyumba yatsopano ya amishonale ndiponso chipinda cha mabuku yatsegulidwa ku Zomba pa September 1, 1998. Imeneyi ndi nyumba yachitatu ya amishonale m’dziko muno. Ili pa Plot Na. CHWO 32, ndipo ili pamsewu wa ku Mangochi, makilomita atatu kuchokera ku Zomba. Chipinda cha mabuku chimenechi chizikhala chotsegula Lachiŵiri ndi Lachinayi kuyambira 7:30 a.m. kufikira 12:00 masana.

◼ Zofalitsa Zatsopano Zimene Zilipo:

Elementary Bible Teachings—Chitumbuka

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena