Kugaŵira Buku la Chidziŵitso
1 “Moyo wosatha ndi uwu,” anatero Yesu m’pemphero kwa Atate wake, “kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha.” (Yoh. 17:3) Imeneyi ndi mfupotu yaikulu kwambiri! Mwa kugwiritsa ntchito buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, tingathandize ena kuphunzira zimene afunikira kuchita kuti akhale ndi moyo kosatha. Kodi tinganenenji kuti tidzutse chidwi chawo ndi kuwasonkhezera kufuna kuŵerenga buku la Chidziŵitso?
2 Mungagwiritsire ntchito ulaliki umene ukusonyeza Baibulo kukhala magwero a chitsogozo chothandiza, mwa kunena kuti:
◼ “Tikukambirana ndi anansi athu za kumene tingapeze chitsogozo chothandiza cholimbanirana ndi mavuto a moyo. Kale anthu ambiri ankayamba achifuna m’Baibulo. Koma tsopano maganizo a anthu asintha; ambiri amakayikira Baibulo, akumaliona ngati buku wamba lolembedwa ndi anthu. Kodi mukuganizapo bwanji? [Yembekezerani yankho.] Pali chifukwa chabwino kwambiri chimene tinganenere kuti Baibulo nlothandiza m’tsiku lathu. [Ŵerengani 2 Timoteo 3:16, 17.] Mapulinsipulo a Baibulo amagwira ntchito kwambiri lerolino monga momwe anachitira pamene Mulungu anauzira kulembedwa kwa Baibulo.” Tsegulani patsamba 16 m’buku la Chidziŵitso, ndi kufotokoza mwachidule za chitsogozo chopindulitsa chopezeka mu Ulaliki wa pa Phiri wa Yesu. Ŵerengani mawu ogwidwa opezeka m’ndime 11 kapena a m’ndime 13. Gaŵirani bukulo, ndipo linganizani za kudzabweranso kuti mudzayankhe funso lakuti, Kodi ifeyo tingapindule motani ndi chidziŵitso chimene chili m’Baibulo?
3 Popeza kuti anthu ambiri amasangalatsidwa ndi nkhani ya pemphero, mungakonde kukambirana za nkhaniyo mwa kufunsa kuti:
◼ “Pokhala ndi zovuta zonse zimene timayang’anizana nazo m’moyo wamakono, kodi muganiza kuti pemphero lingatithandizedi? [Yembekezerani yankho.] Ambiri amati ayandikira kwa Mulungu mwa kupemphera kwa iye ndi kuti kuchita motero kwawapatsa nyonga, imenedi Baibulo limalonjeza. [Tsegulani buku la Chidziŵitso patsamba 156, ndi kuŵerenga Afilipi 4:6, 7.] Komabe, munthu angalingalire kuti nthaŵi zina mapemphero ake sayankhidwa. Mutu uwu ukufotokoza ‘Mmene Mungayandikirire kwa Mulungu.’ [Gaŵirani bukulo, ndipo tchulani chopereka chanthaŵi zonse cha ntchito ya padziko lonse.] Mutu umenewu ukufotokozanso mmene tingamvetsere kwa Mulungu, popeza kuti kulankhula naye sikuli kwa mbali imodzi. Tingadzakambirane zimenezo pamene ndibweranso.”
4 Kodi mungakonde kafikidwe kachindunji kuti muyambitse phunziro? Nayi njira imene ingakhale yabwino kwa inu:
◼ “Tikusonyeza kachitidwe ka kosi ya phunziro la Baibulo lapanyumba laulere. Kodi munachitapo kosi ya Baibulo? [Yembekezerani yankho.] Ndiloleni ndikusonyezeni buku lothandiza kuphunzira limene timagwiritsa ntchito.” Sonyezani buku la Chidziŵitso, tsegulani patsamba 3 kuti mwininyumbayo aone mpambo wa zamkati, ndi kufunsa kuti, “Kodi munaganizapo ponena za zimene Baibulo limanena pankhani izi?” Tsegulani pa mutu umene wasangalatsidwa nawo kwambiri ndi kuŵerenga mitu yake yaing’ono. Fotokozani kuti mukufuna kumsonyeza mwachidule mmene timaphunzirira nkhaniyi pakosi yathu. Kaya phunziro layambidwa kapena ayi, gaŵirani bukulo pachopereka chanthaŵi zonse.
5 Lerolino makamu a anthu akulabadira chidziŵitso cholongosoka chonena za Mulungu woona. (Yes. 2:2-4) Ndi mwayi wathu kuthandiza anthu ambiri monga momwe tingathere kuti aphunzire za Yehova ndi kutsogoleredwa ku moyo.—1 Tim. 2:4.