Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tiyenera kuyesetsa kwambiri kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April ndi May: Masabusikiripishoni a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kapena makope a magaziniwo. Khalani ndi bolosha la Mulungu Amafunanji kaamba ka anthu okondwerera, ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. June: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.
◼ Ofalitsa omwe akufuna kuchita upainiya wothandiza m’April ndi m’May ayenera kuyamba kukonzekera tsopano lino ndipo ayenera kupereka mafomu awo mwamsanga. Zimenezi zidzathandiza akulu kupanga makonzedwe ofunikira a utumiki wakumunda ndi kupeza magazini ndi mabuku ena okwanira. Mayina a anthu omwe avomerezedwa kukhala apainiya othandiza ayenera kulengezedwa kumpingo.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina amene iye wam’sankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa March 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detilo. Mutatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo pambuyo popereka lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ Chikumbutso chidzakhalako Lachinayi, pa April 1, 1999. Ngati mpingo wanu nthaŵi zonse umachita misonkhano Lachinayi, muyenera kuisinthira patsiku lina mlungu womwewo ngati Nyumba ya Ufumu idzakhale isakugwira ntchito. Ngati zimenezi zili zosatheka ndipo Msonkhano wa Utumiki wanu wakhudzidwa, mbali zomwe zili zofunika kwambiri pampingo wanu zingaphatikizidwe mu Msonkhano wa Utumiki wotsatirawo.
◼ Omwe akugwirizana ndi mpingo ayenera kutumiza masabusikiripishoni atsopano ndi ofuna kulembetsanso a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, kuphatikizapo masabusikiripishoni awoawo, kudzera kumpingo.
◼ Sosaite silembera wofalitsa oda ya mabuku. Woyang’anira wotsogoza ayenera kukonza chilengezo chimene chiyenera kuperekedwa mwezi uliwonse asanatumize ku Sosaite oda ya mabuku ampingo ya mwezi ndi mwezi kuti onse amene akufuna kukhala ndi mabuku awoawo adziŵitse mbale wosamalira mabuku. Chonde kumbukirani mabuku amene ali paoda yapadera.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo—Chingelezi
New World Translation (Baibulo la saizi ya pakati, bi12)—Chingelezi
Kukambitsirana za m’Malemba —Chingelezi
◼ Kompakiti Disiki Yatsopano Yomwe Ilipo:
Kingdom Melodies, Volume 5