Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/99 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 12/99 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu December: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. January: Buku lililonse la masamba 192 lofalitsidwa chaka cha 1986 chisanafike lomwe mpingo ungakhale nalo m’sitoko. Mipingo imene ilibe mabuku ameneŵa ingagaŵire buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. February: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetsa kwambiri kuyambitsa maphunziro a Baibulo.

◼ Mipingo iyenera kuyamba kufunsira mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 1999 pofunsira mabuku awo a December. Mabaundi voliyumu adzakhalapo m’Chingelezi. Mpaka pamene mabaundi voliyumu adzakhalapo ndi kutumizidwa, adzaonekera monga “Zoyembekezera” pa mpambo wolongedzera mabuku wa mipingo. Mabaundi voliyumu ndi zinthu zofunsira mwapadera.

◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina amene iye wam’sankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa December 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Mutatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo pambuyo popereka lipoti la maakaunti lotsatira.

◼ Chikumbutso cha chaka cha 2001 chidzakhalako Lamlungu, pa April 8, dzuŵa litaloŵa. Taneneratu zimenezi kuti abale apezeretu maholo kapena kukambirana za holo imene imagwiritsidwa ntchito ndi mipingo ingapo komanso kuti mwina ipezeretu malo ena. Akulu ayenera kugwirizana ndi eni malowo n’kutsimikizira kuti chochitikachi sichidzadodometsedwa ndi zochitika zina za pamalowo kuti Chikumbutsocho chidzachitike mwamtendere ndi mwadongosolo. Popeza kuti chochitikacho n’chapadera, posankha wokamba nkhani ya Chikumbutso, bungwe la akulu liyenera kusankha mkulu yemwe alidi wokhoza bwino, osati kumangosinthana chabe kapenanso osati chaka chilichonse azingokamba munthu m’modzimodzi. Zidzatero pokhapokha ngati pali wodzozedwa amene ndi mkulu wokhoza bwino kukamba nkhani.

◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:

Baibulo—Chicheŵa

Mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda a chaka cha 1951-1985—Chingelezi (Chonde pofunsira nenani achaka chimene mukufuna.)

Yearbook of Jehovah’s Witnesses a chaka cha 1994, 1995, 1997—Chingelezi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena