Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu January: Buku lililonse la masamba 192 lofalitsidwa 1986 isanafike lomwe mpingo ungakhale nalo. Mipingo imene ilibe mabuku ameneŵa ingagaŵire mabuku alionse amene mpingo ungakhale nawo. February: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzachite khama kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April: Makope a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Khalani ndi bulosha la Mulungu Amafunanji kaamba ka anthu okondwerera, ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro apanyumba a Baibulo.
◼ Ofalitsa onse obatizidwa amene adzapezeka pa Msonkhano wa Utumiki wa mlungu wa January 10 adzapatsidwa makadi a Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu ndi makadi a ana awo.
◼ Kuyambira mu February osapyola March 5, oyang’anira dera adzayamba kukamba nkhani yatsopano yapoyera yamutu wakuti “Armagedo Yeniyeni—Chifukwa? Liti?”
◼ Mipingo ikonzekere kudzachita Chikumbutso chaka chino Lachitatu, pa April 19, dzuŵa litaloŵa. Ngakhale kuti nkhani ingayambe mofulumira, kuyendetsa zizindikiro za Chikumbutso sikuyenera kuchitika dzuŵa lisanaloŵe. Fufuzani kwa anthu odziŵa zanyengo kwanuko kuti mutsimikizire nthaŵi yoloŵera dzuŵa m’dera lanu. Ngakhale kuti zimakhala bwino mpingo uliwonse kuchita Chikumbutso pawokha, nthaŵi zina zimenezi sizingatheke. Kumene mipingo ingapo nthaŵi zonse imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mwina mpingo umodzi kapena yoposerapo ingapeze malo ena oti agwiritse ntchito madzulo amenewo. Tikupereka malingaliro akuti, ngati kuli kotheka, mapologalamu akatha pazipita mphindi zosachepera 40 ena asanayambe kuchitira kuti onse apindule mokwanira ndi chochitikacho, kuwapatsa nthaŵi yokwanira yolonjera alendo, kulimbikitsa amene angoyamba kumene kukondwerera. Muyeneranso kulingalira za vuto la kayendedwe ndi malo oimikapo galimotozo, kuphatikizapo kusiya ndi kunyamula anthu. Bungwe la akulu liyenera kusankha makonzedwe amene angakhale abwino kwambiri pampingo wawo.
◼ Nkhani yapoyera yapadera ya nyengo ya Chikumbutso cha 2000 idzakambidwa Lamlungu, pa April 16. Mutu wa nkhani udzakhala wakuti “Chifukwa Chake Mtundu wa Anthu Ukufunikira Dipo.” Autilaini yake idzatumizidwa. Mipingo imene mlungu umenewo idzakhala ikuchezeredwa ndi woyang’anira dera, msonkhano wadera, kapena tsiku la msonkhano wapadera idzakhala ndi nkhani yapaderayi mlungu wotsatira. Palibe mpingo umene uyenera kukhala ndi nkhani yapaderayi lisanafike tsiku la April 16, 2000.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe—Chicheŵa
Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano—Chicheŵa
Mtendere Weni-weni ndi Chisungiko—Zochokera ku Magwero Otani?—Chicheŵa
Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona—Chicheŵa