Tidzaphunzira Buku la Chimwemwe cha Banja
1 Mudzakondwa kudziŵa kuti kuyamba ndi mlungu wa April 17, 2000, tidzaphunzira buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja pa Phunziro la Buku la Mpingo. Palibe ayenera kuphonya pophunzira monga gulu chitsogozo cha m’Malemba chimenechi cha moyo wa banja wachimwemwe. Ndandanda ya phunziro limeneli idzalola kupenda mokwana bwino ndime iliyonse ndi malemba a Baibulo amene ali m’bukumo.
2 Mutu wonse woyamba tidzauphunzira pamlungu woyamba wa phunzirolo, popeza ulibe malemba ambiri osagwidwa mawu. Pachifukwa chomwechonso, mutu 15 tidzauphunzira paphunziro limodzi. Komabe, mitu ina yonse idzagaŵidwa paŵiri, n’kumaphunzira ngati theka la mutu mlungu uliwonse. Choncho, padzakhala nthaŵi yokwana yoŵerenga ndi kukambirana malemba onse osonyezedwa limodzinso ndi kupenda mosamalitsa mmene tingagwiritsire ntchito malemba onse ogwidwa mawu m’ndime iliyonse.
3 Mbali yofunika ya phunziroli idzakhala kukambirana za m’bokosi lophunzitsa pamapeto pa mutu uliwonse. Chotero, tiyenera kugaŵa nthaŵi yokwana yokambirana mafunso ndi malemba osonyezedwa m’bokosimo.
4 Otsogoza Phunziro la Buku la Mpingo akulimbikitsidwa kukonzekera phunziro lawo mosamalitsa ndi kulimbikitsa onse a m’gulu lawo, kuphatikizapo atsopano, kuti azikonzekera bwino, kupezekapo nthaŵi zonse, ndi kutengamo mbali.—om-CN 74-6.