Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu June: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. July ndi August: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabulosha a masamba 32 ali m’munsiŵa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Mabulosha a Buku la Anthu Onse, ndi Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? angagaŵiridwe pamene kuli koyenera kutero. September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.
◼ Tikufuna kukumbutsa mipingo yonse kuti pakamafika pa 6 mwezi wotsatira, chonde izikhala itatumiza ku Sosaite malipoti ampingo autumiki wakumunda (S-1). Komanso chonde izionetsetsa kuti lipotilo n’lokwanira, mwa kusonkhanitsa malipoti a anthu onse amene analoŵa muutumiki kuti tizikhala ndi lipoti lolondola la utumiki wakumunda. Kwapezeka kuti mipingo ina imatumiza ku Sosaite maola ochepa kwambiri. Chonde gwiritsani ntchito maenvulopu olembedwa kuti REPORT DESK kaamba ka malipoti a S-1 okha.
◼ Zofalitsa Zimene Zilipo:
“All Scripture Is Inspired of God”—Chingelezi
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo—Chicheŵa
Samalirani Ulosi wa Danieli—Chicheŵa
Kaseti Yatsopano Imene Ilipo:
Kuyamikira Choloŵa Chathu Chauzimu—Chingelezi
Kaseti Yatsopano ya Vidiyo Imene Ilipo:
Our Whole Association of Brothers—Chingelezi (Vidiyo imeneyi imasonyeza mmene gulu lonse la abale limagwirira ntchito mogwirizana posonkhana, kulalikira, ndi kuthandizana m’nthaŵi za masoka, ngakhale ali m’mikhalidwe yosiyana kwambiri).