Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/00 tsamba 2
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 7/00 tsamba 2

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu July ndi August: Lililonse la mabulosha a masamba 32 ali m’munsiŵa angagwiritsidwe ntchito: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, What Happens to Us When We Die?, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Mabulosha a Buku la Anthu Onse, ndi Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo ilikodi? angagaŵiridwe poyenera kutero. September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. October: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukapeza anthu achidwi paulendo wobwereza, mungagaŵire masabusikiripishoni.

◼ Kuyambira mwezi wa September, oyang’anira dera adzakamba nkhani yapoyera yamutu wakuti, “Ulamuliro wa Anthu—Uyesedwa pa Muyeso.”

◼ Kope lino la Utumiki Wathu wa Ufumu lili ndi ndandanda yonse ya maphunziro a buku la Samalani Ulosi wa Danieli! Mungaichite fotokope n’kuiika m’buku lanu lophunzirira kuti muzitha kuona mosavuta.

◼ Ngati mukufuna kupereka ndalama zothandizira pamavuto ogwa mwadzidzidzi, mungatumize thandizo lanulo ku Sosaite, kumene amasunga ndalama za ntchito imeneyi. Adiresi yake ndi: Watch Tower Society, P.O. Box 30749, Lilongwe 3. (Onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 1986 tsamba 20-2.) Chonde musatumize zovala, ziwiya, kapena katundu ku Sosaite kapena ku malo kumene kwagwa masoka ngati Sosaite kapena komiti yachithandizo sinakupempheni kutero. Izi zidzapangitsa kuti katundu wachithandizo aziyenda mwandondomeko ndiponso azigaŵidwa bwino.

◼ Masiku a Msonkhano Wachigawo wa Chingelezi wachaka chino wa mutu wakuti “Akuchita Mawu a Mulungu” asintha. Ndipo ali motere:

Blantyre September 8-10

Lilongwe August 11-13

Masiku amisonkhano yachigawo ina yonse ali monga momwe analengezera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2000. Tikupepesa kaamba ka mavuto ena alionse amene angabwere chifukwa cha kusintha kumeneku.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena