‘Menyani Nkhondo Yabwino ya Chikhulupiriro’
1 Mtumwi Paulo analangiza Timoteo ‘kumenya nkhondo yabwino ya chikhulupiriro.’ (1 Tim. 6:12, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Paulo mwiniyo anakhala mogwirizana ndi mawu ameneŵa. Kumapeto kwa moyo wake, analankhula motsimikiza kuti iye anali atamenya nkhondo yabwino. (2 Tim. 4:6-8) M’njira zonse, anachita utumiki molimba mtima, ndi mopirira. Mwa kutsanzira chitsanzo chake, tingakhutire kuti tikuchita zomwe tingathe pankhondo yathu ya chikhulupiriro chachikristu.
2 Chitani Khama Limene Likufunika: Paulo anagwira ntchito molimbika mu utumiki. (1 Akor. 15:10) Ifenso timatero pofuna anthu onse amene ali oyenera m’gawo lathu. (Mat. 10:11) Kuti tifikire ena mwa anthu ameneŵa, kungafune kudzuka m’maŵa kukachitira umboni kwa anthu oyenda mumsewu. Kapena zingafune kugwira ntchito madzulo ndithu kapena kutangoyamba kumene kuda kuti tikakumane ndi anthu akamabwerera kunyumba zawo.
3 Pamafunika kudzilanga komanso ndandanda yabwino kuti tizifika m’nthaŵi yabwino pokakumana ndi gulu lathu la phunziro la buku kaamba ka utumiki wakumunda. Mwachitsanzo m’mayiko ena, pamapeto a mlungu, anthu ena a m’banja la Beteli amayenda ola limodzi popita kukachita nawo utumiki pamodzi ndi mipingo imene anagaŵiridwa. Komanso, tingasilire ofalitsa ndi mabanja ena mu mpingo wathu amene amayenda mtunda wautali koma amafika msanga. Zitsanzo zoterezi za anthu akhama ndi olinganiza bwino zinthu n’zofunika kuzitsanzira.
4 Tiyenera kusonkhezeredwa kubwererako konse kumene tapeza anthu achidwi. Ngakhale pogaŵira magazini mumsewu kapena mwamwayi, tiyenera kuyesetsa kutenga adiresi kapena nambala ya telefoni ya munthuyo. Choncho titha kudzayesetsa kulankhula naye n’cholinga chokulitsa chidwi ndi kuyambitsa phunziro la Baibulo.
5 Khalani Wokhazikika mu Utumiki: Paulo anali wakhama ndi wolimbikira mu ulaliki. (Aroma 15:19) Nanga inuyo? Kodi mumapita mokhazikika mu utumiki? Kodi mwezi uno mwapitako mu utumiki wakumunda? Ochititsa phunziro la Buku la Mpingo akufuna kuona kuti aliyense wa m’gulu lawo akuchita nawo utumiki m’mwezi wa August. Adzakuthandizani kuti muchite zimenezi.
6 Mwa kutsanzira Paulo pochirikiza mokwanira uthenga wabwino, tidzapitiriza ‘kumenya nkhondo yabwino ya chikhulupiriro.’