Lingalirani Ntchito Zodabwitsa za Mulungu
1 Kwa masiku atatu abwino, tinali pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Akuchita Mawu a Mulungu.” Tinachotsa malingaliro athu pazimene timachita m’moyo watsiku ndi tsiku n’kuwaika pantchito zodabwitsa za Yehova. Msonkhano unakonzedwa n’cholinga chokulitsa chikhulupiriro chathu mwa Mulungu ndi m’Mawu ake, kulimbitsa unansi wathu ndi iye, ndiponso kuwonjezera changu chathu pa utumiki. Kodi tikupindula motani ndi zinthu zimene tinaphunzitsidwa?—Yoh. 13:17.
2 Mabanja Mverani Mawu a Mulungu: Nkhani yosiyirana ya mutu wakuti “Mverani Mawu a Mulungu” inatithandiza kupenda mkhalidwe wauzimu wa mabanja athu. Ana amakonda kuphunzira. Choncho, makolo oopa Mulungu analimbikitsidwa kupanga phunziro la Baibulo la banja kukhala maziko a banja lolimba mwauzimu. Mitu ya mabanja yambiri ikuphunzira ndi ana awo bulosha latsopano lakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! Zimenezi ziwathandiza kukhala ndi unansi wabwino komanso wolimba ndi Yehova. Makolo, aphunzitseni ana anu mmene angapeŵere kukhumudwitsa Mulungu. Sonyezani kuti mumam’konda komanso mumakonda zochita zake. (Sal. 103:2) Chitirani zinthu limodzi poika ndi kukwanitsa zolinga zauzimu ndiponso potumikira Yehova mokwanira.
3 Mawu a Mulungu Akuunikira Njira Yathu: Tinali osangalala kwambiri kulandira buku latsopano la Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse 1. Kodi gawo loyambali mwaliŵerenga kufika pati? Buku la Yesaya limaneneratu za ziweruzo zoopsa pa mitundu yosapembedza komanso madalitso abwino a Ufumu kwa anthu a Mulungu. (Yes. 34:2; 35:10) Limalimbitsanso chikhulupiriro ndi chidaliro mwa Yehova ndiponso mmene amachitira zinthu.—Yes. 12:2-5.
4 Poŵerenga Ulosi wa Yesaya 1, mutha kuona kumayambiriro kwenikweni mmene Yesaya anakhalirabe wokhulupirika kwa Yehova atazingidwa ndi zoipa. Atafunsidwa kukhala mthenga wa Mulungu, Yesaya anayankha kuti: “Ndine pano; munditumize.” (Yes. 6:8) Kulingalira za mzimu wake wofunitsitsa kudzakulimbikitsani kupitiriza kulalikira uthenga wabwino, kutenga nawo mbali mokwanira m’ntchito yochitira “umboni kwa anthu a mitundu yonse.”—Mat. 24:14.
5 Kulingalira kwathu ntchito za Yehova kudzawonjezera ukulu wake. Choncho nyadirani mwayi wokhala akuchita Mawu a Mulungu!