Kuthandiza Ana Athu Kukhalabe m’Choonadi: Mbali Yachitatu—Mwa Phunziro la Baibulo Lokhazikika
1 Mbali yachiŵiri ya nkhani ino inafotokoza chifukwa chake makolo sayenera kuchedwa kuyambitsa ana awo kuloŵa mu utumiki. Moyo wauzimu wa ana anu ndiwo maziko enieni othandizira ana anuwo kupita patsogolo. Ndipo zimenezo zimadalira kuchititsa kwanu phunziro la Baibulo la banja, lokhazikika ndi logwira mtima. M’mbali yachitatu ndi yachinayi, tidzafotokoza mbali imeneyi ya kuthandiza ana athu kukhalabe m’choonadi.
2 N’zoona kuti si mwana aliyense amene angadzakhale mtumiki wa Yehova. Zili choncho chifukwa chakuti munthu aliyense, zilibe kanthu analeredwa bwino chotani m’choonadi, ayenera kusankha yekha ngati akufunadi kutumikira Yehova. Sitingakakamize chokhumba chimenecho mwa iwo. (Lingalirani chitsanzo cha Isake ndi Ismayeli, Yakobo ndi Esau.) Mulimonse mmene ana angaphunzitsidwire panyumba ndipo ngakhale makolo awo atakhala ochita bwino chotani mwauzimu, panthaŵi inayake anawo adzayenera kusankha chimene eniakewo akufuna kuchita. Ngati asiya choonadi, chikhale chifukwa cha mtima wawo wosamva, osati chifukwa chakuti makolo awo kapena mpingo sunawaphunzitse ndi kuwasamalira ayi. −1 Yoh. 2:19.
3 Phunziro la Baibulo la Banja: Pachifukwa chimenechi, tikupempha makolo kuwonjezera khama lawo poyesetsa kuthandiza ana awo kutumikira Yehova. Kuchititsa phunziro la banja lokhazikika ndi chinthu chofunika kwambiri. Nthaŵi imene mumaiwonongera paphunzirolo ndi yamtengo wapatali kwabasi. Poganizira udindo wanu wa m’Malemba wakuti “muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye,” tikuona kuti ndi chinthu chofunika kwambiri. (Aef. 6:4) Ngati simunakhazikitsebe phunziro la banja, teroni mlungu womwe uno mosalephera. Ngati mumachititsa, chitani zimenezo mokhazikika mlungu uliwonse. Musalole china chilichonse kusokoneza mbali yofunika kwambiri imeneyi ya zochitika zanu zauzimu.
4 Ndiponso, phunziro lanu la banja siliyenera kungokhala mbali ya mafunso ndi mayankho basi kuti muone ngati ana anu amadziŵa kuyankha mafunso. Liyenera kukhala latanthauzo ndi losangalatsa. Onetsetsani kuti, malingana ndi msinkhu wawo ndi nzeru zawo, anawo akumayesetsa kupereka mayankho m’mawu awoawo. Pendani ngati iwo amakhulupiriradi zimene akunenazo, mwa kuwafunsa mafunso ngati aŵa: Kodi iweyo umakhulupirira chiyani? Kodi uganiza kuti zimenezi zidzachitikadi? Kodi izi n’zimene udzafuna kuchita? Lolani kuti alankhule zakukhosi kwawo. Musawadzudzule ngati sakuyankha mmene mukufunira. Koma yesetsani zolimba kukhomereza choonadi m’mitima yawo. (Deut. 6:4-7) Ikani maganizo anu ndi moyo wanu wonse pa kuphunzitsa kumeneku. Komanso, pemphani Yehova nthaŵi zonse kuti akutsogolereni, makamaka ngati zikuvuta kuti ana anu muwatsogolere m’njira ya choonadi.
5 Kuyambira pamene ali makanda, muyenera kulimbikitsa m’mitima ya ana anu chikhumbo champhamvu chotumikira Yehova. Mwakutero, adzafuna kukhala ofalitsa Ufumu ngakhale asanafike zaka khumi. Mveketsani kwa iwo kuti umenewo ndi mwayi wodabwitsa komanso cholinga chosiririka chabwino kwambiri. Musaleke kulimbikitsa mwa iwo chikhumbo champhamvu chimenechi. Mmene inuyo mumatengera ntchito yolalikira ndi chinthu chofunika kwambiri. Ngati mumazengereza kutengamo mbali, ngati simusangalala nayo, ngati mumalalikira mosachokera pansi pamtima, ana anu adzazindikira zimenezo. Iwo sadzatengera mawu anu koma adzatsanzira inu amene. Kuti muphunzitse ana anu, mudzafunikira kudziphunzitsa inu eni komanso kuonetsetsa kuti utumiki wa Yehova mumauona motani.
6 Ntchito Yomanga: Cholinga chanu ndicho kumanga ana anu kukhala ophunzira a Kristu. Tamverani zimene Paulo akunena pa 1 Akorinto 3:10: “Koma yense ayang’anire umo amangira . . . ” Kenako akupitiriza kusonyeza kuti n’kutheka kuti mwina tikumanga ndi zomangira zosalimba ndi zosakhalitsa, zonga ngati mitengo, udzu, ndi ziputu? Kunena za banja, zimenezi zikutanthauza kuti mtundu wa kaphunzitsidwe ndi chitsanzo chimene tikupereka ndi zosakhala bwino. Kusiyana ndi zimenezo, tikufuna kumanga ana athu kuti akhale atumiki a Yehova mwa kugwiritsa ntchito zomangira zolimba monga golidi, siliva, ndi miyala ya mtengo wapatali. Kunena kwina, tilimbikitse mikhalidwe yofunika monga chikhulupiriro, chikondi, kudzipereka kwa Mulungu ndi kupirira. Mikhalidweyi idzalimbikitsa ana athu kutumikira Yehova ndi kukhalabe mu utumiki wake. Ngati zomangira zosagwira moto sizinamangidwe mwa ana athu kenako iwo n’kusiya choonadi, tamverani zimene Paulo akunena kuti zimachitika m’vesi ya 15: “Ngati ntchito ya wina itenthedwa, zidzawonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto.” Zomangira zosalimba mwa ana athu zingasonyeze kuti mwina ife enife tikupereŵera m’chikondi chathu kwa Yehova ndi pakudzipereka kwathu kwa iye. Imeneyitu ndi nkhani yoopsa kwambiri.−onani w84 8/1 mas. 8-12.
7 Popeza kuti ana amatengera chitsanzo cha makolo awo pa zabwino ndi zoipa zomwe, mukhozanso kuona maganizo a ana anu pankhani ya kulambira Yehova kukhala chithunzithunzi cha maganizo a inu eni. Kuli ngati kudziyang’ana pa galasi. Ngati mukuona vuto linalake m’kupembedza kwa ana anu, pangakhale kufunikira kwakuti inuyo mumenyere nkhondo kukulitsa chikondi chanu kwa Yehova ndi kudzipereka kwanu kwa iye, komanso kuthandiza ana anu kuchita chimodzimodzi.
8 M’mbali yotsatira ya nkhani imeneyi, tidzakambirana mmene tingagonjetsere zopinga zina zolepheretsa kuchititsa maphunziro a banja
(Yapitirizidwa pa tsamba 4)
Ana(Yopitirizidwa)